Pitirizani “Kubala Zipatso Zambiri”
1 Yesu ananena mophiphiritsira kuti iye ndiye mpesa weniweni, Atate wake ndi Mlimi, ndipo otsatira ake odzozedwa ndiwo nthambi zobala zipatso. Pofotokoza ntchito ya Mlimi wophiphiritsa, Yesu anatsindika kufunika kokhalabe olumikizika kwambiri kumpesa. (Yoh. 15:1-4) Phunziro limene tikupezapo pamenepa n’loti, aliyense amene ali pa ubwenzi wabwino kwambiri ndi Yehova ayenera kukhala ngati nthambi yobala zipatso ya “mpesa weniweni,” womwe ndi Yesu Khristu. Tifunikira kupitirizabe kubala kwambiri “zipatso za mzimu” ndiponso zipatso za Ufumu.—Agal. 5:22, 23; Mat. 24:14; 28:19, 20.
2 Zipatso za Mzimu: Anthu ena angadziwe kuti tikuchita bwino mwauzimu kapena ayi makamaka poona mmene timasonyezera zipatso za mzimu. Kodi mumayesetsa kukhala ndi zipatso za mzimu wa Mulungu mwa kuphunzira ndi kusinkhasinkha za Mawu a Mulungu nthawi zonse? (Afil. 1:9-11) Musazengereze kupempherera mzimu woyera, umene ungakupangitseni kukhala ndi makhalidwe amene amalemekeza Yehova ndiponso amene angakuthandizeni kuti mupitirizebe kuchita bwino mwauzimu.—Luka 11:13; Yoh. 13:35.
3 Kukhala ndi zipatso za mzimu kungatithandizenso kukhala atumiki achangu kwambiri. Mwachitsanzo, chikondi ndi chikhulupiriro zimatilimbikitsa kupatula nthawi kuti tilalikire nawo nthawi zonse, ngakhale kuti ndife otanganidwa. Ndipo makhalidwe monga mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, kufatsa, ndi kudziletsa amatithandiza kuchita zinthu mwanzeru anthu akamatitsutsa. Ndiyeno, chimwemwe chimatithandiza kusangalalabe ndi utumiki wathu ngakhale pamene anthu sakumvetsera zimene tikuwauza.
4 Zipatso za Ufumu: Timafunikiranso kubala zipatso za Ufumu. Zimenezi zimaphatikizapo kupereka “nsembe ya chitamando, ndiyo chipatso cha milomo yathu, inde, milomo imene imalengeza dzina [la Yehova] poyera.” (Aheb. 13:15) Timachita zimenezi mwa kulengeza uthenga wabwino mwachangu ndiponso mokhulupirika. Kodi inuyo mukuyesetsa kubala zipatso za Ufumu zambiri mwa kuchita bwino muutumiki wanu?
5 Yesu ananena kuti otsatira ake okhulupirika adzabala zipatso zochuluka mosiyanasiyana. (Mat. 13:23) Motero, tisadziyerekezere ndi anthu ena koma tizipereka kwa Yehova zonse zimene ifeyo tingathe. (Agal. 6:4) Kuunika bwinobwino moyo wathu mogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu kungatithandize kupitiriza kulemekeza Yehova mwa “kubala zipatso zambiri.”—Yoh. 15:8.