Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/07 tsamba 5
  • Bokosi la Mafunso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Bokosi la Mafunso
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Nkhani Yofanana
  • Ana Akamagwiritsa Ntchito Intaneti Zimene Makolo Ayenera Kudziwa
    Galamukani!—2008
  • Ana Akamagwiritsa Ntchito Intaneti Zimene Makolo Angachite
    Galamukani!—2008
  • Kodi Ndingapeŵe Bwanji Zoopsa pa Intaneti?
    Galamukani!—2000
  • Kuthandiza Achinyamata Kukhalabe Okhulupirika
    Galamukani!—2007
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
km 7/07 tsamba 5

Bokosi la Mafunso

◼ Kodi kucheza pa Intaneti ndi anthu omwe sitikuwadziwa n’koopsa motani?

Pa Intaneti pali malo ambiri omwe anakonzedwa n’cholinga choti anthu azicheza mwa kulemberana mauthenga. Pamalo ambiri amenewa, anthu amatha kufotokoza za moyo wawo ndi kuikapo zithunzi. Kenako, anthu amene amaona zinthu zimenezi angalembere anthu omwe anaziikapo. Achinyamata ndi amene amakonda kwambiri malo amenewa, ndipo achinyamata ena mumpingo agwiritsa ntchito malowa kucheza ndi anthu omwe amati ndi a Mboni za Yehova.

N’zosavuta kwa munthu yemwe tikulemberana naye mauthenga pa Intaneti kuti atinamize ponena za moyo wake, unansi wake ndi Yehova, kapena zolinga zake. (Sal. 26:4) Munthu yemwe anganene kuti ndi wa Mboni za Yehova kwenikweni angakhale munthu wosakhulupirira, wochotsedwa, kapena ngakhale wampatuko. (Agal. 2:4) Ndipo zikuoneka kuti anthu ambiri ogona ana amagwiritsa ntchito malo amenewa kuti apeze omwe angawagwirire.

Ngakhale kuti ifeyo tikuonadi kuti anthu omwe tikulemberana nawo mauthengawo amachita bwino mumpingo, n’zosavuta kuti tiyambe kucheza za zinthu zosayenera. Zili choncho chifukwa choti nthawi zambiri anthu akamacheza ndi munthu yemwe sanakumanepo naye maso ndi maso amamasuka kunena zinthu zilizonse. Ndipo angaonenso kuti zimene akulemberana sizingadziwike kwa anthu ena monga makolo awo kapena akulu. N’zomvetsa chisoni kuti achinyamata ambiri a m’mabanja achikhristu agwidwa mu msampha umenewu moti akhala akulankhula nkhani zotukwana. (Aef. 5:3, 4; Akol. 3:8) Achinyamata ena, pamalo amenewo alembapo mayina antchedzera otukwana, aikapo zithunzi zoyambitsa chilakolako chogonana ndiponso mavidiyo olaula anyimbo.

Chifukwa cha zimene tafotokozazi, makolo ayenera kuyang’anira ana awo akamagwiritsa ntchito kompyuta. (Miy. 29:15) Zingakhale zoopsa kwambiri kulola munthu yemwe sitikumudziwa kulowa m’nyumba yathu kapena kum’siya yekha kuti acheze ndi ana athu. Mofanana ndi zimenezi, n’koopsa kwambiri kuti ana athu kapena ifeyo tizicheza pa Intaneti ndi anthu omwe sitikuwadziwa, ngakhale atanena kuti ndi Mboni za Yehova.—Miy. 22:3.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena