Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 10/07 tsamba 1
  • Limbikitsani Osauka

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Limbikitsani Osauka
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Nkhani Yofanana
  • Posachedwapa, Sikudzakhalanso Mmphaŵi!
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Tsanzirani Yesu Poganizira Osauka
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Mapeto a Umphaŵi Ayandikira
    Galamukani!—1998
  • Kodi Amphaŵi Adzafunikira Kuyembekezera Kwautali Wotani?
    Nsanja ya Olonda—1995
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
km 10/07 tsamba 1

Limbikitsani Osauka

1 Yesu ankadera nkhawa osauka. Nthawi zina ankawapatsa chakudya ndi kuwachiritsa mozizwitsa, koma maganizo ake anali pa kuwalalikira “uthenga wabwino.” (Mat. 11:5) Utumiki wachikhristu masiku ano umathandizanso anthu osauka ndi ena onse.—Mat. 24:14; 28:19, 20.

2 Chiyembekezo Chotsimikizirika: Nthawi zambiri atsogoleri amatchalitchi amauza anthu osauka kuti akhoza kulemera ngati apereka ndalama zambiri ku tchalitchi. Komabe, Baibulo limaphunzitsa kuti ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene udzathetsa umphawi ndi mavuto onse a anthu. (Sal. 9:18; 145:16; Yes. 65:21-23) Tikasonyeza anthu osauka zimene Baibulo limaphunzitsadi, timawalimbikitsa ndi kuwathandiza kudziwa Mulungu ndi kuyamba kumulambira.—Mat. 5:3.

3 M’nthawi ya Yesu, Afarisi sankawerengera anthu osauka moti ankawanyoza kuti ndi ‘am-ha·’aʹrets, kapena kuti “anthu apansi.” Komabe, Yesu ankaona “mwazi wawo” kapena kuti moyo wawo kukhala “wa mtengo” wapatali. (Sal. 72:13, 14) Tingatsanzire Yesu ndi ‘kuchitira chifundo’ anthu osauka mwa kuwakomera mtima ndi kuwamvera chisoni. (Miy. 14:31) Tisanyoze kapena kupewa kulalikira anthu amene amakhala m’madera a anthu osauka. Anthu ambiri amene akulabadira uthenga wa Ufumu ndi osauka.

4 Athandizeni Panopo: Kuphunzitsa anthu osauka a m’gawo lathu mfundo za m’Baibulo kungawathandize kuchepetsako umphawi. Mwachitsanzo, Baibulo limaletsa kuledzera, njuga, ulesi, kusuta, ndi zinthu zina zimene zimapangitsa munthu kukhala wosauka. (Miy. 6:10, 11; 23:21; 2 Akor. 7:1; Aef. 5:5) Malemba amalimbikitsa anthu kukhala oona mtima ndi kugwira ntchito ndi ‘moyo wawo wonse,’ ndipo izi n’zimene mabwana amafuna kwa antchito awo. (Akol. 3:22, 23; Aheb. 13:18) Ndipotu, pakufufuza kwina anapeza kuti mabwana ambiri akamalemba antchito, amafuna anthu oona mtima ndi okhulupirika.

5 Yehova amasamala za mavuto a anthu osauka. Yesu Khristu posachedwapa adzapulumutsa “waumphawi wofuulayo.” (Sal. 72:12) Komabe tikuyembekezera nthawiyo, ndi mwayi wathu kuthandiza ena, ndi osauka omwe, kukhala ndi chiyembekezo chopezeka m’Baibulo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena