Limbikitsani Anthu Osweka Mtima
1 Nthawi yathu ino anthu ambiri akufunikira kulimbikitsidwa kuposa ndi kale lonse. Potsatira chitsanzo cha Mfumu yathu, Khristu Yesu, nafenso tiyenera kulimbikitsa “osweka mtima.”—Yes. 61:1.
2 Zimene Tingachite Kuti Tilimbikitsire Ena: Tizionetsetsa kuti ulaliki wathu ndi wolimbikitsadi. Tiyenera kuchepetsa kulankhula za ziphunzitso zonyenga zimene anthu amakhulupirira ndi zoipa zomwe zikuchitika padzikoli, n’kumalankhula kwambiri za choonadi cha m’Malemba ndi chiyembekezo cholimbikitsa cha malonjezo a Mulungu. Zimenezi sizikutanthauza kuti tileke kukambirana ndi anthu za Aramagedo. Tikutero chifukwa chakuti ntchito yathu ndi yolalikira za “chaka chokomera Yehova, ndi tsiku lakubwezera la Mulungu wathu,” komanso ‘kuchenjeza woipa aleke njira yake yoipa.’ Ngakhale zili choncho, tikamachenjeza anthu za Aramagedo ndi zotsatira zake, sikuti cholinga chathu ndi kuphimba uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ayi.—Yes. 61:2; Ezek. 3:18; Mat. 24:14.
3 Kulalikira Khomo ndi Khomo: Kawirikawiri timaona anthu osweka mtima chifukwa cha matenda, imfa ya wokondedwa wawo, kupanda chilungamo kapena mavuto azachuma. Monga anthu otsatira Khristu, ‘timamvera chifundo’ anthu amene timakumana nawo muutumiki wathu. (Luka 7:13; Aroma 12:15) Ngakhale kuti tingawerenge ndi kufotokozera munthu lemba limodzi kapena awiri okhudzana ndi vuto lake, tiziyesetsa kumupatsa mpata munthuyo wofotokoza maganizo ake ndipo tizimvetsera. (Yak. 1:19) Tikamachita zimenezo tizitha kuwalimbikitsadi anthu.
4 Panthawi yoyenerera pokambiranapo, tinganene kuti, “Ndikufuna ndikambirane nanu mawu ena olimbikitsa a m’Baibulo.” Tifunika kusamala kuti tisamangotsutsa chilichonse cholakwika chimene munthuyo anganene. M’malo mwake cholinga chathu chachikulu chizikhala kulimbikitsa anthu ndi Malemba. Kuti tichite zimenezi, tingagwiritse ntchito buku lakuti Kukambitsirana za m’Malemba, masamba 79-82, pamutu wakuti “Chilimbikitso.” Kapena tingapatse mwininyumba kapepala kamutu wakuti Chitonthozo kwa Opsinjika Maganizo ndi kukambirana naye nkhani zolimbikitsa za m’kapepalako.
5 Tizifuna Mipata Yolimbikitsira Ena: Kodi tikudziwa munthu aliyense woyandikana naye nyumba, wogwira naye ntchito, mnzathu wa kusukulu kapena wachibale amene akufunika kulimbikitsidwa? Bwanji osayesetsa kuwayendera anthu amenewo kunyumba kwawo n’cholinga chokawalimbitsa ndi Malemba? Kudziwa chifukwa chake munthuyo akufunikira kulimbikitsidwa kungatithandize kuti tikonzekere bwino. Pofuna kuchita zimenezi, ena amalemba makalata kapena kuimba foni. Chikondi chenicheni chidzatilimbikitsa kumvera ena chisoni ndi kuwalimbikitsa ndi Malemba.—Luka 10:25-37.
6 Zoonadi, ife tatumidwa kulimbikitsa olira, kutsitsimula anthu osweka mtima, ndi kuwapatsa chiyembekezo cha tsogolo labwino. Ichi ndicho chilimbikitso chimene anthu padziko lonse akufunikira. Kulankhula mosangalala za zinthu zabwino zambiri zimene Mulungu walonjeza, kumalimbikitsa anthu a mtima wabwino ndiponso kuwapatsa chiyembekezo. Tiyeni nthawi zonse tizikumbukira kuti tifunikira kulimbikitsa osweka mtima.