Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/08 tsamba 1
  • Khalani Mtumiki Wopita Patsogolo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Khalani Mtumiki Wopita Patsogolo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Mungaphunzitsire Ofalitsa Atsopano Kulalikira
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
  • Kodi Mukukwaniritsa Mbali Zonse za Utumiki Wanu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Khalani ndi Zolinga Zauzimu
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Kodi Tingatani Kuti Tizikondabe Kulalikira?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
km 4/08 tsamba 1

Khalani Mtumiki Wopita Patsogolo

1 Atate wathu wakumwamba amasangalala kwambiri atumiki ake akamapita patsogolo mwauzimu. Kupita patsogolo kumeneku kumaphatikizapo kukula mwauzimu ndi kukhala atumiki ogwira mtima a uthenga wabwino. Paulo analimbikitsa Timoteyo yemwe anali woyang’anira, kuti apitirize kukhala wakhama n’cholinga chakuti kupita patsogolo kwake kuonekere. (1 Tim. 4:13-15) Tonsefe ngakhale amene takhala ofalitsa kwa nthawi yaitali tiyenera kuyesetsa kukulitsa luso lathu muutumiki.

2 Khalani ndi Zolinga: Kuti munthu apite patsogolo amafunika kukhala ndi zolinga. Kodi zina mwa zolinga zimene tingakhale nazo ndi ziti? Mwina tingayese kukulitsa luso lathu logwiritsa ntchito Baibulo, lomwe ndi lupanga lathu lauzimu. (Aef. 6:17) Mwinanso tingafune kukulitsa luso lathu pa ulaliki wina, monga ulaliki wa mumsewu, wapatelefoni kapena wam’gawo la malonda. Tingafunenso kupanga maulendo obwereza ogwira mtima kwambiri. Cholinga china chabwino kwambiri chingakhale kukulitsa luso lathu loyambitsa ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo.

3 Zomwe Zingakuthandizeni: Misonkhano ya mpingo, makamaka Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ndi Msonkhano wa Utumiki, imakonzedwa n’cholinga chotithandiza kukhala atumiki opita patsogolo. Tingapindule kwambiri tikamachita khama kukonzekera ndi kupezeka pa misonkhanoyi ndiponso kugwiritsa ntchito malangizo ake.—2 Akor. 9:6.

4 Kuti tipite patsogolo, timafunikanso kuthandizana. (Miy. 27:17) Kumvetsera mosamala ulaliki wa anthu amene tikuyenda nawo muutumiki kungatithandize kupita patsogolo. Kuwonjezera pamenepo, woyang’anira gulu lathu la phunziro la buku angakonze zoti tithandizidwe. Ndi madalitso aakulu kuti mpainiya kapena wofalitsa wodziwa bwino utumiki atithandize kukhala ogwira mtima ndi kusangalala kwambiri ndi utumiki wathu. Kodi m’gulu lathu la phunziro la buku muli wofalitsa watsopano? Mwina tingam’pemphe kuti tiyende naye muutumiki.

5 Utumiki wachikhristu ndi wofunika kwambiri pantchito zonse zomwe zikuchitika masiku ano. Tikamapereka kwa Yehova “nsembe ya chitamando,” timafuna kum’patsa nsembe zabwino kwambiri. (Aheb. 13:15) Tikamayesetsa kukhala opita patsogolo muutumiki, tingakhale antchito ‘opanda chochita nacho manyazi, owalondoloza bwino mawu a choonadi.’—2 Tim. 2:15.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena