Mmene Mungaphunzitsire Ofalitsa Atsopano Kulalikira
1. Kodi munkamva bwanji nthawi yanu yoyamba kulowa mu utumiki?
1 Kodi mukukumbukira mmene munkamvera nthawi yanu yoyamba kulowa mu utumiki wakunyumba ndi nyumba? N’kutheka kuti munali ndi mantha kwambiri. Ngati munali limodzi ndi amene ankakuphunzitsani Baibulo kapena wofalitsa wina, muyenera kuti munasangalala kwambiri kuti akukuthandizani. Tsopano mwazolowera utumikiwu, choncho mungathe kuphunzitsa ofalitsa atsopano kulalikira.
2. Kodi ofalitsa atsopano amafunika kuphunzitsidwa chiyani?
2 Ofalitsa atsopano amafunika kuphunzira mmene angayambire kukambirana ndi eninyumba, kugwiritsa ntchito Baibulo polalikira, kupanga maulendo obwereza, ndi kuyambitsa komanso kuchititsa maphunziro a Baibulo. Ayeneranso kuphunzira njira zosiyanasiyana zolalikirira monga ulaliki wa m’misewu komanso kulalikira anthu m’malo amene amagwira ntchito. Mungawathandize kuti azichita bwino mbali zimenezi powapatsa chitsanzo komanso malangizo oyenera.
3. Kodi tingathandize bwanji ena mwa chitsanzo chathu?
3 Apatseni Chitsanzo: Yesu anawasonyeza ophunzira ake zimene anayenera kuchita polalikira. (Luka 8:1; 1 Pet. 2:21) Mukapangana kuti mulowe mu utumiki ndi wofalitsa watsopano, konzani ulaliki wosavuta woti wofalitsa watsopanoyo angathe kutsatira. Mwina mungakonze ulalikiwu potengera zitsanzo zimene zimakhala m’mabuku athu. Kenako, muuzeni kuti inuyo mulalikira pakhomo limodzi kapena awiri oyambirira kuti iye amve zimene munganene. Mukachoka pakhomo lililonse mungamufunse kuti afotokoze zimene waona kuti n’zothandiza kwambiri pa ulaliki wanuwo. Zimenezi zingamuthandize kuti aone ubwino woyenda ndi munthu wina mu utumiki ndipo zingakhale zosavuta kwa iye kugwiritsa ntchito malangizo amene mungam’patse iyeyo akalalikira.
4. Kodi tingathandize bwanji wofalitsa watsopano pambuyo poti tamvetsera ulaliki wake?
4 Apatseni Malangizo: Yesu anawapatsanso ophunzira ake malangizo oti azitsatira polalikira. (Mat. 10:5-14) Inunso mungathe kuthandiza wofalitsa watsopano pochita zomwezi. Nthawi yake yoti alalikire ikakwana, mvetserani mwatcheru. Kenako mukachoka pakhomolo, musazengeleze kutchula ndiponso kumuyamikira pa zimene wachitadi bwino, ngakhale patakhala zina ndi zina zofunika kuti akonze. Musafulumire kum’patsa malangizo pa zimene walakwitsa. Mwina analakwitsa chifukwa cha mantha chabe. Choncho yembekezerani kaye kuti muone ngati angakonze yekha zolakwikazo pakhomo lotsatira. Muyeneranso kukumbukira kuti wofalitsa aliyense amakhala ndi luso losiyana ndi la ena, ndipo nthawi zambiri pamakhala njira zambiri zolondola zochitira chinthu chimodzi.—1 Akor. 12:4-7.
5. Kodi tiyenera kunena chiyani tikafuna kupereka malangizo kwa wofalitsa watsopano?
5 Nthawi zina wofalitsa watsopano angakufunseni nzeru. Koma ngati sanakufunseni chilichonse, inuyo chitanipo kanthu. Kodi mungatani kuti muchite zimenezi popanda kumukhumudwitsa? Ofalitsa ena amene achita utumikiwu kwa nthawi yaitali amangofunsa kuti, “Kodi mukudziwa njira ina imene mukanafotokozera zimenezi?” kapena, “Kodi mukuona kuti zayenda bwanji?” Mwinanso mungathe kungonena kuti, “Nditangokhala kumene wofalitsa zinkandivuta kuchita zakutizakuti, koma chimene chinandithandiza ndi chakutichakuti.” Nthawi zina mungachite bwino kuwerengera limodzi mfundo zina zimene zili m’buku la Kukambitsirana. Kuti asaone ngati mukum’panikiza, mungachite bwino kum’patsa malangizo pa mbali imodzi yokha imene sanachite bwino pa ulaliki wake.
6. Pa nkhani yochita utumiki, kodi chitsulo chimanola bwanji chitsulo chinzake?
6 Chitsulo Chimanola Chitsulo Chinzake: Paulo analimbikitsa Timoteyo, yemwe anali atalalikira uthenga wabwino kwa nthawi yaitali, kuti apitirize kuchita khama pophunzitsa komanso kuti apitirize kupita patsogolo. (1 Tim. 4:13, 15) N’kutheka kuti nanunso mwakhala mukuchita utumiki kwa nthawi yaitali, komabe muyenera kupitiriza kuwonjezera luso lanu. Muziphunzira pa zimene ofalitsa anzanu amachita, ngakhale pa zimene ofalitsa amene sanazolowere utumikiwu amachita. Komanso muzikhala wokonzeka kuthandiza ena mokoma mtima, makamaka ofalitsa atsopano, kuti nawonso akhale atumiki a uthenga wabwino aluso.—Miy. 27:17.