Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 5/08 tsamba 4
  • Mungathe Kukhala Olemera

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mungathe Kukhala Olemera
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Nkhani Yofanana
  • Madalitso a Utumiki wa Upainiya
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Madalitso a Utumiki Waupainiya
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Kodi Mukufunitsitsa Kukhala Wolemera Mwauzimu?
    Galamukani!—2007
  • Kodi Tsopano Khomo Lochita Upainiya Lakutsegukirani?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
km 5/08 tsamba 4

Mungathe Kukhala Olemera

1. Kodi n’chifukwa chiyani muyenera kuganizira zoyamba upainiya wokhazikika?

1 Kodi mukufuna moyo wabwino ndi wosangalala? Kodi mumasangalala kuthandiza ena? Kodi mukufuna kutumikira Yehova mowonjezereka? Ngati mwayankha kuti inde pa lililonse la mafunsowa, muyenera kuganizira zoyamba upainiya wokhazikika. Koma musanatero, mufunikabe kuganizira zinthu monga, udindo wanu wosamalira banja kapena maudindo ena a m’Malemba, thanzi lanu ndiponso zovuta zina pamoyo wanu.

2. Tchulani madalitso ena auzimu amene apainiya okhazikika amapeza?

2 Mouziridwa ndi Mulungu, Solomo analemba mawu amene amasonyeza kugwirizana kwa madalitso a Yehova ndi chuma chakuthupi. (Miy. 10:22) Masiku ano, madalitso a Yehova amalemeretsa, koma makamaka mwauzimu. Ndipo apainiya okhazikika amapeza chuma chauzimu chochuluka. Mwachitsanzo, iwo amakhala osangalala kwambiri chifukwa chokhala opatsa mwa ‘kuwombola nthawi’ imene akanachitira zinthu zina. (Akol. 4:5; Mac. 20:35) Yehova amaona ndi kuyamikira zimene iwo amachita chifukwa cha chikondi chawo. ‘Chuma chakumwamba’ chimenechi sichingawonongeke ngakhale patapita nthawi. (Mat. 6:20; Aheb. 6:10) Ndipo apainiya akamapitiriza kukhala ndi ‘diso lolunjika chimodzi,’ ndi kukhulupirira kuti Yehova aziwapatsa zofunikira pamoyo, ubwenzi wawo ndi iye umakhala wolimba. —Mat. 6:22, 25, 32; Aheb. 13:5, 6.

3. Kodi pali kusiyana kotani pakati pa kufunafuna chuma chauzimu ndi kufunafuna chuma chakuthupi?

3 Kawirikawiri, anthu amene amafunafuna chuma chakuthupi amagwera “m’zilakolako zambiri zopanda nzeru ndi zopweteka.” (1 Tim. 6:9, 10; Yak. 5:1-3) Koma madalitso a Yehova sabweretsa zimenezi. Kuthera nthawi yochuluka muutumiki kumathandiza apainiya okhazikika kukhalabe olimba mwauzimu, komanso kuganizira zinthu zofunika kwambiri. (Afil. 1:10) M’bale wina yemwe anali injiniya, anasiya ntchito yakeyo chifukwa inkamudyera nthawi ndipo anayamba upainiya. Iye anati: “Ntchito yanga inkandipanikiza kwambiri. Koma upainiya sundipanikiza. Panopa ndimathandiza anthu ndi kuwaphunzitsa choonadi. Ndipo zimenezi zimandisangalatsa ndi kundikhutiritsa kwambiri.”

4. Kodi apainiya okhazikika amadalitsidwa bwanji chifukwa chokhala dalitso kwa ena?

4 Mungakhale Dalitso kwa Ena: Masiku ano, aliyense amakumana ndi mavuto chifukwa tili mu “nthawi yovuta.” (2 Tim. 3:1) Kulikonse anthu akufunikira kwambiri chiyembekezo. Olengeza Ufumu amasangalala akaona anthu amene anali ndi nkhawa chifukwa chopanda chiyembekezo akusintha, n’kukhala osangalala chifukwa cholabadira uthenga wabwino. Zimenezi zimabweretsa chimwemwe chochuluka kwa apainiya okhazikika, amene amathera maola oposa 800 chaka chilichonse akugwira ntchito yopulumutsa anthu imeneyi.—1 Tim. 4:16.

5, 6. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kukhala mpainiya wokhazikika?

5 Kodi mwakhala mukuganizira mwakuya zokhala mpainiya wokhazikika? Kuti muchite upainiya, mungafunike ‘kudziwombolera nthawi yoyenerera’ ku zinthu zomwe si zofunika kwambiri. (Aef. 5:15, 16) Ambiri achita zimenezi ndipo achepetsa zina ndi zina pamoyo wawo. Ndipo kutero kwawathandiza kuti asamathere nthawi yambiri pantchito yolembedwa, n’cholinga chakuti akhale ndi nthawi yambiri yochita zinthu za Ufumu. Kodi inunso mungasinthe zinthu zina pamoyo wanu kuti muyambe upainiya?

6 Pemphani nzeru kwa Yehova kuti muthe kukonza pulogalamu yabwino. (Yak. 1:5) Kodi mutatero mungapeze madalitso otani? Mungapeze chuma chochuluka chauzimu. Ndiponso, Yehova angakudalitseni mwa kukupatsani zinthu zakuthupi zimene mukufunikira. (Mat. 6:33) Anthu amene amayesa Yehova pankhani imeneyi, amalandira ‘mdalitso wakuti amasoweka malo akuulandira.’—Mal. 3:10.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena