Lemekezani Yehova Tsiku Lililonse
1. Kodi atumiki a Mulungu akulimbikitsidwa kuchita chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani?
1 Mfumu Davide anafotokoza kuti anali wofunitsitsa kutamanda Yehova “masiku onse,” mpaka muyaya. (Sal. 145:2, 7, 21) Nafenso tili ndi zifukwa zomveka zolemekezera Yehova tsiku lililonse.—Sal. 37:10; 145:14, 18; 2 Pet. 3:13.
2. Kodi mabanja angatani kuti azilemekeza Yehova tsiku lililonse?
2 Panyumba Pathu: Tili ndi mabuku ambiri abwino otithandiza pokambirana lemba latsiku, pochita Kulambira kwa Pabanja ndiponso pokonzekera misonkhano yampingo. Mabanja ambiri amaonetsetsa kuti tsiku lililonse apeze nthawi yoti adyere limodzi chakudya. Zimenezi zimathandiza kuti azicheza mwachifatse, momasuka ndiponso zimawapatsa mwayi wolemekeza Yehova. Ndipo zimathandiza kwambiri makolo polera ana awo kuti akule ‘m’maleredwe ndi m’chilangizo cha Yehova.’—Aef. 6:4; Deut. 6:5-7.
3. Kodi tikakhala ndi abale athu timakhala ndi mpata wotani?
3 Tikakhala ndi Abale: Tikakhala ndi abale athu mu utumiki wakumunda kapena pamisonkhano, timakhala ndi mwayi waukulu wolemekeza Yehova. (Miy. 15:30; Afil. 4:8; Aheb. 13:15) Popeza kuti tonse timakonda Yehova, sizingativute kukambirana nkhani zomuyamikira chifukwa cha zinthu zabwino zimene amatichitira.—Sal. 106:1.
4. Kodi mungalemekeze Yehova panthawi ziti?
4 Polankhula ndi Anthu Ena: Ngakhale kuti zochitika pamoyo wathu sizingatilole kulalikira tsiku lililonse za Yehova ndiponso zolinga zake, kungolalikira mwachidule kwa anzathu akuntchito, akusukulu ndiponso oyandikana nawo, kungathandize anthu amitima yabwino kuti akhale ndi chiyembekezo. (Sal. 27:14; 1 Pet. 3:15) Mlongo wina analalikira mayi wina yemwe anakwera naye ndege. Mayiyu anasangalala ndipo analimbikitsidwa kwambiri ndi zimene anamva kwa mlongoyu moti anam’patsa adiresi ndiponso nambala yake ya foni kuti adzalankhulanenso nthawi ina. Pamene mavuto akuchulukirachulukira ndiponso zinthu zikuipiraipira padzikoli, atumiki a Yehova akupitirizabe kulalikira “uthenga wabwino wa zinthu zabwino,” kwa anthu omwe akufunitsitsa kumva. Zimenezi zimathandiza anthu ena kukhala ndi chiyembekezo ndiponso zimawalimbikitsa kulemekeza Yehova.—Yes. 52:7; Aroma 15:11.
5. N’chifukwa chiyani tikufunitsitsa kulemekeza Yehova, ndipo zimenezi zingakwaniritse chiyani?
5 Yehova ayenera kuti amasangalala kwambiri kumva atumiki ake akumulemekeza tsiku lililonse. Mofanana ndi zolengedwa za Yehova zimene timaziona, ifenso tingam’lemekeze tsiku lililonse panyumba pathu, mumpingo ndiponso polalikira kwa anthu ena.—Salmo 19:1-4.