Kodi Ndine Woyenerera Kulalikira?
1. Kodi n’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira kuti ndife oyenerera kulalikira?
1 Ngati munakhalapo ndi vuto lokayikira zoti ndinu woyenera kulalikira musadandaule. Kuti mukhale woyenerera kulalikira simufunikira kukhala munthu wophunzira kwambiri kapena waluso lachibadwa. Ophunzira ena m’nthawi ya Yesu ankanenedwa kuti anali “osaphunzira ndiponso anthu wamba.” Komabe iwo ankalalikira mogwira mtima uthenga wabwino chifukwa choti anafunitsitsa ndi mtima wonse kutsanzira Yesu.—Mac. 4:13; 1 Pet. 2:21.
2. Tchulani zinthu zina zokhudza kaphunzitsidwe ka Yesu.
2 Kaphunzitsidwe ka Yesu: Yesu ankaphunzitsa m’njira yosavuta kumva, yotsatirika komanso yothandiza. Mafunso ake, zitsanzo zake ndiponso mawu okopa amene ankayambira nkhani zake ankachititsa anthu kumvetsera mwachidwi. (Mat. 6:26) Iye ankawasonyeza anthu chidwi chenicheni. (Mat. 14:14) Chinanso, Yesu ankalankhula molimba mtima ndiponso mosonyeza kuti ali ndi ulamuliro. Ankatero chifukwa chodziwa kuti Yehova ndi amene anam’patsa ntchito imeneyi komanso mphamvu zoti aikwaniritse.—Luka 4:18.
3. Kodi Yehova amatithandiza bwanji kuti tikwaniritse utumiki wathu?
3 Yehova Amatithandiza: Kudzera m’Mawu ake komanso gulu lake, Mlangizi Wamkulu amatiphunzitsa zonse zimene tiyenera kudziwa kuti tithe kulalikira bwinobwino uthenga wabwino. (Yes. 54:13) Yehova anachititsa kuti zimene Yesu ankachita pophunzitsa zilembedwe, motero tingathe kuphunzirapo kanthu n’kumamutsanzira. Yehova amatipatsa mzimu wake woyera ndipo amatiphunzitsa pamisonkhano ya mpingo. (Yoh. 14:26) Komanso watipatsa ofalitsa anzathu aluso amene angatithandize kukulitsa luso lathu.
4. N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayika kuti ndife oyenerera kulalikira uthenga wabwino?
4 Palibe chifukwa chokayikira kuti ndife oyenerera kulalikira chifukwa “kukhala kwathu oyenerera bwino lomwe kuchokera kwa Mulungu.” (2 Akor. 3:5) Tikamadalira Yehova n’kumagwiritsa ntchito bwino zinthu zimene watipatsa mwachikondi chake, ‘timakhala oyenera mokwanira, okonzeka bwino lomwe kuchita ntchito iliyonse yabwino.’—2 Tim. 3:17.