Khalidwe Lofunika Kwambiri la Mphunzitsi Wabwino
1. Tchulani khalidwe lofunika kwambiri la mphunzitsi wabwino.
1 Kodi n’chiyani chimachititsa munthu kukhala mphunzitsi wabwino wa mawu a Mulungu, Baibulo? Kodi ayenera kukhala wophunzira kwambiri? Wodziwa zinthu zambiri? Waluso lachibadwa? Ayi, chofunika kwambiri ndi khalidwe limenenso limakwaniritsa Chilamulo. Khalidwe limeneli ndi lomwenso limadziwikitsa ophunzira a Yesu ndiponso ndi khalidwe lalikulu komanso lokopa kwambiri pa makhalidwe akuluakulu a Yehova. (Yoh. 13:35; Agal. 5:14; 1 Yoh. 4:8) Khalidwe limeneli ndi chikondi. Aziphunzitsi abwino amakhala achikondi.
2. N’chifukwa chiyani tiyenera kukonda anthu?
2 Muzikonda Anthu: Mphunzitsi Waluso, Yesu, ankakonda anthu ndipo zimenezi zinachititsa kuti anthu azimumvetsera. (Luka 5:12, 13; Yoh. 13:1; 15:13) Ngati timafunira zabwino anthu, tidzalalikira nthawi ina iliyonse imene tapeza mpata. Sitidzalephera kulalikira chifukwa cha chizunzo ndiponso kusowa chidwi kwa anthu. Tidzasonyeza chidwi chenicheni anthu amene timawalalikira ndiponso tidzasintha ulaliki wathu kuti ugwirizane ndi zosowa zawo. Tidzakhala okonzeka kupatula nthawi yocheza ndi wophunzira Baibulo aliyense payekha komanso yokonzekera zimene tikaphunzire ndi munthu aliyense.
3. Kodi kukonda choonadi cha m’Baibulo kungatithandize bwanji mu utumiki?
3 Muzikonda Choonadi cha m’Baibulo: Nayenso Yesu ankakonda choonadi cha m’Baibulo ndipo ankachiona kuti ndi chuma chamtengo wapatali. (Mat. 13:52) Ngati timakonda choonadi, tidzalankhula mwachidaliro ndipo zimenezi zikhoza kuchititsa omvera athu kukhala ndi chidwi. Chikondi chimenechi chidzatichititsa kuganizira kwambiri za kufunikira kwa uthenga wathu ndipo sitidzadandaula ndi zofooka zathu komanso sitidzachita mantha tikakhala mu utumiki.
4. Kodi tingatani kuti tizikonda kwambiri anthu?
4 Kulitsani Chikondi: Kodi tingatani kuti tizikonda kwambiri anthu? Tizitengera chikondi chimene Yehova ndi Mwana wake amasonyeza komanso tiziona mmene anthu a m’gawo lathu akuvutikira mwauzimu. (Maliko 6:34; 1 Yoh. 4:10, 11) Kuphunzira Baibulo patokha ndiponso kuganizira mozama zimene taphunzirazo kungatithandizenso kuti tizikonda kwambiri choonadi cha m’Baibulo. Chikondi ndi khalidwe limodzi mwa makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa. (Agal. 5:22) Choncho, tingapemphe Yehova kuti atipatse mzimu woyera ndiponso kuti atithandize kukulitsa chikondi. (Luka 11:13; 1 Yoh. 5:14) Ndiyetu kaya tinaphunzira kwambiri kapena ayi, timadziwa zinthu zambiri kapena ayi, tili ndi luso lachibadwa kapena ayi, tikhoza kukhala mphunzitsi wogwira mtima ngati tingamakonde ena.