Ntchito Imene Imakhala ndi Zotsatira Zabwino
Chaka chinonso tidzagawira timapepala toitanira anthu ku msonkhano wachigawo patatsala milungu itatu kuti msonkhano wathu uchitike. Mpake kuti timayenera kugwira ntchitoyi chifukwa imakhala ndi zotsatira zabwino kwambiri. Anthu amene amalandira timapepalati n’kubwera ku msonkhanowu, nthawi zambiri amagoma ndi nkhani za m’Baibulo zimene zimakambidwa pa msonkhano komanso amachita chidwi ndi abale ndi alongo amene amatumikira m’madipatimenti osiyanasiyana. Amachitanso chidwi ndi khalidwe lathu labwino komanso mgwirizano umene timakhala nawo pa misonkhanoyi. (Sal. 110:3; 133:1; Yes. 65:13, 14) Komabe kodi ntchito yathu yoitanira anthu ku misonkhanoyi imakhaladi ndi zotsatira zabwino, makamaka tikaganizira kuti anthu ena amene timawaitana amakhala kutali ndi malo a msonkhano?
Pambuyo pa msonkhano wachigawo wa 2011, ofesi ya nthawi ina inalandira kalata yochokera kwa mayi wina yemwe anapeza kapepala komuitanira ku msonkhano pachitseko cha nyumba yake. Nthawi zambiri, mayiyu ankabisala a Mboni akafika panyumba yake. Iye analemba kuti: “Ndili ndi nyumba yabwino komanso mwamuna wabwino, ndipo ndinkaganiza kuti zinthu zimenezi zingandithandize kukhala wosangalala. Komabe, sindinkasangalala ndipo moyo wanga unalibe cholinga chilichonse. Choncho, Loweruka ndinaganiza zopita ku msonkhanowo ndipo ndinanyamuka pa galimoto n’kuyenda mtunda wa makilomita 320 kuti ndikafike pamalo a msonkhano.” Mayiyu anasangalala kwambiri ndi pulogalamu ya tsikuli moti anaimbira foni mwamuna wake n’kumuuza kuti agona komweko n’cholinga choti achite nawonso msonkhanowu Lamlungu. Iye anati: “Ndinamvetsera nkhani zonse ndipo ndinakumana ndi a Mboni za Yehova ambirimbiri. Ndinasangalala kwambiri ndi msonkhanowu moti sindinkafuna kuti uthe.” Atabwerera kwawo, anayamba kuphunzira Baibulo ndipo patatha miyezi inayi yokha, anakhala wofalitsa wosabatizidwa. Mayiyu anati: “Ndimasangalala kwambiri kuti ndinapeza kapepala kondiitanira ku msonkhano kaja pachitseko cha nyumba yanga ndipo panopa ndimaona kuti moyo wanga ulidi ndi cholinga chenicheni.”
Anthu ena amene adzapatsidwe timapepalati adzabwera ku msonkhano wachigawo. Choncho, tiyeni tonse tidzagwire mwakhama ntchito yofunika imeneyi. Mudzabwere ndi timapepala totsala ku msonkhanowu kuti mudzatigwiritse ntchito polalikira mwamwayi.
[Chithunzi patsamba 5]
Kodi Tidzagawira Bwanji Timapepalati?
Kuti tidzakwanitse kugawira timapepalati m’gawo lathu lonse, ndi bwino kulankhula mwachidule. Mwina tinganene kuti: “Takupezani. Tikugwira ntchito imene ikuchitika padziko lonse yogawira anthu timapepala towaitanira ku msonkhano. Choncho kapepala kanu ndi aka. Zonse zokhudza msonkhanowu zili pakapepala kameneka.” Muyenera kukhala wansangala pamene mukugawira timapepalati. Ngati mukugawira timapepalati kumapeto kwa mlungu, mungagawirenso magazini kwa munthu amene wasonyeza chidwi.