Ntchito ya Padziko Lonse Yolengeza za Msonkhano Wachigawo Wakuti “Tsatirani Khristu!”
Ofalitsa Adzagawiranso Kapepala Kapadera
1 Chaka chatha anthu ambiri anachita chidwi ndi ntchito ya padziko lonse yolengeza za msonkhano wachigawo wakuti “Chipulumutso Chayandikira.” Anthu amene anaitanidwa ndi kubwera ku msonkhanowu, anadzionera okha koyamba mmene phwando lauzimu la Mboni za Yehova limakhalira. Nawonso anasangalala kukhala pamodzi ndi abale athu achikhristu ogwirizana ndiponso okondana. (Sal. 133:1) Pofuna kuthandiza anthu ambiri kuti adzabwere ku msonkhano wachigawo wakuti “Tsatirani Khristu!” tikhalanso ndi ntchito yogawira kapepala kapadera padziko lonse.
2 Zimene Zinachitika Chaka Chatha: Malinga ndi malipoti omwe tinalandira padziko lonse, ntchito yolengeza za msonkhano wachigawo wakuti “Chipulumutso Chayandikira,” inayenda bwino kwambiri. M’madera ambiri, anthu ananena zabwino za ntchito yathu. Mwachitsanzo, kudziko lina, nyuzipepala ina inafalitsa nkhani yaikulu yofotokoza za ntchito imeneyi ndipo inati: “A Mboni m’dera lino ali kalikiliki kugwira ntchito nthawi yaitali, kuyenda maulendo aatali, ndi kulankhula mofulumira kuti afikire munthu aliyense nthawi idakalipo.” Mumzinda wina, ntchito yogawira kapepala kameneka inakopa chidwi cha atolankhani ndipo anailemba kwambiri m’manyuzipepala. Nyuzipepala zosachepera zitatu zinalemba nkhani zabwino za ntchito imeneyi msonkhano usanachitike. M’nyuzipepala ina ya Lamlungu, mtolankhani wina analemba nkhani zingapo zazitali kupitirira masamba awiri. Nyuzipepalayo inafotokoza zambiri zokhudza zimene timakhulupirira, ubale wathu, ntchito yogawira kapepala ka msonkhano, ndi za msonkhanowo. Wofalitsa atafika pa khomo lina ndi kupereka kapepala koitanira anthu ku msonkhano, mwininyumba anamudula mawu ndi kumuuza kuti, “Ee! ndangowerenga kumene za nkhaniyi m’nyuzipepala.” Mwininyumba wina anati: “Posachedwapa, ndimawerenga za inuyo, ndipo mwafika kale? Kapepala kanga kali kuti?” Kenako anati: “Inu a Mboni za Yehova mukuchita ntchito yabwino kwambiri.”
3 Anthu ambiri achidwi anabwera ku msonkhano ali ndi timapepala tawo m’manja. Ena anayenda pa galimoto kuchokera ku mizinda yakutali kuti akakhale nawo pazigawo zina za msonkhano. Chifukwa cha khama lathu, anthu ambiri anabwera ku msonkhano. Mwachitsanzo, kudziko lina anthu amene anafika pa msonkhano anawonjezereka ndi 27 peresenti kuposa chaka chinacho.
4 Kufola Gawo: Mungayambe kugawira timapepalati patatsala milungu itatu kuti msonkhano wanu uyambe. Yesetsani kufola gawo lonse la mpingo wanu. Mipingo imene ili ndi gawo lalikulu, ofalitsa angasiye kapepala mwanzeru panyumba imene sanapeze munthu kutatsala mlungu umodzi kuti msonkhano uyambe. Mipingo iyenera kuyesetsa kugawira timapepala tawo tonse ndi kufola gawo lonse. Timapepala tonse totsala tingathe kugwiritsidwa ntchito ndi apainiya mumpingo mwanu.
5 Zimene Munganene: Mukafika pa khomo, munganene kuti: “Tili pa ntchito yogawira kapepala koitanira anthu kumsonkhano wofunika kwambiri. Ntchito imeneyi ikuchitika pa dziko lonse. Eni, kapepala aka. Zambiri zokhudza msonkhanowu zafotokozedwa mmenemu.” Kuti mugawire timapepalati kwa anthu ambiri, lankhulani mwachidule. Koma ngati mwininyumba ali ndi mafunso, mutha kuwayankha. Mukapeza munthu wachidwi, lembani ndipo mubwerereko mwamsanga.
6 Ndithudi, kutsatira Khristu n’kofunika kwambiri. (Yoh. 3:36) Msonkhano wachigawo ukubwerawu udzatithandiza tonse kuchita zimenezo. Chifukwa cha ntchito imeneyi yolengeza za msonkhano wachigawo wakuti “Tsatirani Khristu!” tikukhulupirira kuti anthu ambiri adzalalikidwa. Choncho, chitani changu kuitana anthu ambiri. Yehova adalitse khama lanu pamene mukugwira nawo ntchito ya padziko lonse imeneyi.