Ntchito Yapadera ya Padziko Lonse Yolengeza za Msonkhano Wachigawo Wakuti “Chipulumutso Chayandikira”
Ofalitsa mu Mpingo Uliwonse Agawire Timapepala Tapadera
1 Kuyambira m’nthawi ya masika mu 2006 ku Chigawo Chakumpoto kwa dziko lapansili n’kupitirira mpaka pamapeto pa misokhano yonse yachigawo, padziko lonse padzakhala ntchito yapadera yolengeza za misonkhanoyi. Misonkhanoyi idzachitika m’mayiko pafupifupi 155. Ntchitoyi idzaphatikizapo misonkhano yachigawo yapadera yomwe akonza kuti idzachitike m’mayiko a Germany, Czech Republic, ndi Poland m’mwezi wa July ndiponso mlungu woyamba wa August 2006.
2 Popeza tili kumapeto kwa masiku otsiriza, misonkhano yachigawoyi, yomwe ikufotokoza za lonjezo la Mulungu lodzapulumutsa anthu m’dziko loipali, idzakhala yachikoka kwa anthu a mtima wabwino. Uthenga wa misonkhanoyi udzawalimbikitsa kuganizira za zinthu zimene zidzachitike m’tsogolo. Pofuna kupatsa anthu ambiri mwayi wodzamva nawo uthenga wolimbikitsa ndi wopatsa chiyembekezo, mipingo yoposa 98,000 ya Mboni za Yehova ikulimbikitsidwa kudzalengeza nawo mwakhama za msonkhano wachigawo womwe mpingowo waitanidwako.
3 Mipingo idzalandira timapepala tokwanira toitanira anthu ku msonkhanowu, moti wofalitsa aliyense angathe kudzalandira timapepala 50. Apainiya a mumpingo wanu angagawire timapepala tina tonse totsala. Pa mpingo uliwonse, ntchito yapaderayi idzayamba kutatsala milungu itatu kuti likwane tsiku loyamba la msonkhano womwe mpingowo udzapiteko. Izi zidzathandiza kuti timapepalato tigawidwe m’gawo lalikulu, mwinanso gawo lonse, la mpingowo.
4 Tikukulimbikitsani kuti ngati n’kotheka kapepalako kadzaperekedwe pamanja kwa mwininyumba aliyense. Komabe, ngati panyumba ina palibe munthu, mungathe kukaika bwinobwino pachitseko. M’pofunika kudzachita khama kwambiri kuti timapepala tonse tidzagawidwe m’milungu itatu.
5 Tikukhulupirira kuti chifukwa cha khama lathu padziko lonse polengeza za msonkhano wachigawo wakuti “Chipulumutso Chayandikira,” tidzapereka umboni wamphamvu kwambiri. Tikupemphera kuti Yehova adzadalitse khama lanu pantchito yapadera ya padziko lonse imeneyi.