Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/12 tsamba 3-6
  • Misonkhano Yathu Yachigawo Imafotokoza Mfundo za Choonadi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Misonkhano Yathu Yachigawo Imafotokoza Mfundo za Choonadi
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Nkhani Yofanana
  • Masiku Atatu Otsitsimulidwa Mwauzimu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • Khalidwe Lathu Labwino Limalemekeza Mulungu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Misonkhano Yachigawo Ndi Nthawi Imene Timalambira Mulungu Mosangalala
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
  • “Khalani Ndi Khalidwe Labwino Pakati pa Anthu a M’dzikoli”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
km 6/12 tsamba 3-6

Misonkhano Yathu Yachigawo Imafotokoza Mfundo za Choonadi

1. Kodi pa nthawi ya zikondwerero, Aisiraeli ankakambirana mfundo za choonadi zotani?

1 Kale, Aisiraeli ankasonkhana pa zikondwerero katatu pa chaka. Nthawi zambiri banja lonse linkapita ku Yerusalemu ngakhale kuti amuna okha ndiwo ankayenera kukhala nawo pa zikondwererozi. (Deut. 16:15, 16) Zikondwerero zimenezi zinkawapatsa nthawi yoganizira ndiponso kukambirana mfundo zofunika za choonadi. Kodi ankakambirana zotani pa zikondwererozi? Mfundo imodzi imene ankakambirana ndiponso kuiganizira inali yakuti Yehova ndi wowolowa manja ndiponso wachikondi. (Deut. 15:4, 5) Mfundo ina inali yakuti Yehova ndiye anali woyenera kuwatsogolera ndiponso kuwateteza. (Deut. 32:9, 10) Aisiraeli ankaganiziranso mfundo yakuti azichita zinthu mwachilungamo chifukwa ankatchedwa ndi dzina la Yehova. (Deut. 7:6, 11) Chimodzimodzi masiku ano, misonkhano yathu yachigawo imatithandizanso kwambiri.

2. Kodi msonkhano wachigawo wa chaka chino udzatithandiza motani kumvetsa mfundo za choonadi?

2 Msonkhanowu Udzatithandiza Kumvetsa Bwino Mfundo za Choonadi: Pa misonkhano yathu yachigawo, timasangalala ndi nkhani, masewero, zitsanzo ndiponso nkhani zokhala ndi mbali yofunsa. Zinthu zimenezi zimatithandiza kumvetsa bwino mfundo za choonadi cha m’Baibulo n’kuzigwiritsira ntchito pa moyo wathu. (Yoh. 17:17) Panopo, abale agwira kale ntchito yaikulu pokonzekera msonkhano wa chigawo wa chaka chino. Gulu la Yehova lakonza msonkhano umene ndi wothandiza kwambiri pothana ndi mavuto amene anthu padziko lonse akukumana nawo. (Mat. 24:45-47) Kodi mukufuna kudzamvetsera nkhani zimene zidzakambidwe pa msonkhanowu?

3. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tidzapindule ndi msonkhano umenewu?

3 Komabe, kuti tidzapindule ndi msonkhanowu tiyenera kudzapezeka masiku onse atatu n’kumamvetsera mwatcheru. Pemphani abwana anu kuntchito kuti adzakupatseni nthawi yoti mudzapite kumsonkhanowu. Pa nthawi ya msonkhano, muzidzagona nthawi yabwino kuti muzidzakhala tcheru kumsonkhanowu. Anthu ambiri amaona kuti kuyang’ana munthu amene akukamba nkhani ndiponso kulemba mfundo zachidule kumawathandiza kuti akhale tcheru. Mudzaonetsetse kuti foni yanu isadzasokoneze anthu ena pamsonkhano. Pewani kulankhulana, kutumizirana mameseji pafoni kapena kudya msonkhano uli mkati.

4. Kodi makolo angachite chiyani kuti athandize ana awo kuti adzapindule ndi msonkhanowu?

4 Pa nthawi ya Chikondwerero cha Misasa chomwe chinkachita m’chaka cha 7 chilichonse, Aisiraeli ndi mabanja awo ankasonkhana kuti adzamve Chilamulo chikuwerengedwa. Iwo ankakhala limodzi ndi “ana” awo “kuti amvetsere ndi kuphunzira.” (Deut. 31:12) Zimakhala zolimbikitsa kuona mabanja atakhalira limodzi pamsonkhano ndiponso ana awo akumvetsera mwachidwi. Madzulo aliwonse msonkhano ukatha, mungakambirane mfundo zimene munasangalala nazo kumsonkhanowu. Baibulo limafotokoza kuti: “Uchitsiru umakhazikika mumtima mwa mwana.” Choncho, makolo ayenera kusamalira ana awo ngakhale ana okulirapo pa nthawi yopuma masana komanso kumalo amene akugona. Makolo sayenera ‘kulekerera’ ana awo kuchita zopulupudza.—Miy. 22:15; 29:15.

5. Kodi tizivala motani kuti tikometsere choonadi pamene tili kumsonkhano?

5 Makhalidwe Athu Abwino Amakometsera Choonadi: Makhalidwe athu abwino pamene tili kudera kumene kukuchitikira msonkhano amakometsera choonadi. (Tito 2:10) Tikavala baji ya msonkhano, anthu amadziwa za msonkhano wathu komanso zimathandiza kuti abale athu atidziwe mosavuta. Zimenezi zimatithandizanso kulalikira mosavuta kwa anthu amene takumana nawo. Anthu amene amakhala kudera limene kukuchitikira msonkhano amaona kuti anthu amene avala mabaji a msonkhano avala bwino ndiponso modzilemekeza osati kuvala mosadzilemekeza monga mmene anthu m’dzikoli amavalira. (1 Tim. 2:9, 10) Choncho, pa nthawi ya msonkhano tizionetsetsa kuti tikuvala ndiponso kudzikongoletsa moyenera. N’kosayenera kuvala kabudula ndiponso tisheti kumsonkhano. Ngakhale msonkhano utachitikira pagalaundi, tiyenera kuvalabe modzilemekeza. Ngati tikufuna kuvala zovala zina madzulo msonkhano ukatha n’kupita kukayendayenda, tiyenera kukumbukira kuti tili kumsonkhanobe ndipo tivale modzilemekeza.

6. Kodi tingatani kuti tidzasangalale ndi ubale wathu wachikhristu pamsonkhano?

6 Kuzikondwerero zapachaka, Aisiraeli ochokera kumadera ndi mayiko osiyanasiyana ankalimbikitsana, ndipo zimenezi zinkalimbikitsa umodzi. (Mac. 2:1, 5) Pa nthawi ya misonkhano yachigawo, anthu amaona mgwirizano wathu wachikhristu. Paradaiso wathu wauzimu ameneyu amachititsa anthu amene amationa kutisirira kwambiri. (Sal. 133:1) M’malo mochoka kukagula chakudya chamasana, ndi bwino kubwera ndi chakudya chathu chamasana kuti tikhale ndi nthawi yocheza ndi abale ndi alongo athu amene takhala nawo pafupi.

7. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kugwira nawo ntchito pamsonkhano ngati tingathe?

7 Nthawi zambiri anthu amachita chidwi ndi mmene misonkhano yathu imakonzedwera ndiponso mmene zinthu zimayendera pamisonkhanoyi. Iwo amachita chidwi kwambiri makamaka akadziwa kuti ntchito yonse imene imachitika pamisonkhano imeneyi imagwiridwa ndi anthu ongodzipereka. Kodi mungathe ‘kudzipereka’ kuti mudzagwire nawo ntchito pamsonkhano wachigawo wa chaka chino? (Sal. 110:3) Nthawi zambiri onse m’banja amadzipereka kuti aphunzitse ana awo kukhala ndi mtima wothandiza ena. Ngati ndinu wamanyazi, kugwira nawo ntchito pamsonkhano kungakuthandizeni kudziwana ndi abale ndi alongo ena. Mlongo wina ananena kuti: “Ine ndinkangodziwa anthu a m’banja mwathu ndi anthu ena ochepa basi. Sindinkadziwa anthu ambiri kumsonkhanoko. Koma nditathandiza nawo pa ntchito yoyeretsa, ndinadziwana ndi abale ndi alongo ambiri. Ndinasangalala kwambiri.” Kupeza abale ndi alongo atsopano ocheza nawo pamene tikugwira nawo ntchito pamsonkhano wachigawo kumasangalatsa kwambiri. (2 Akor. 6:12, 13) Ngati simunadziperekepo kugwira nawo ntchito pamsonkhano, funsani akulu kuti akuuzeni zimene mungachite kuti mudzagwire nawo ntchitoyi.

8. Kodi anthu adzaitanidwa motani kuti adzakhale nawo pamsonkhano wachigawo?

8 Itanani Ena Kuti Adzamve Choonadi: Monga mmene takhala tikuchitira m’mbuyomu, chaka chinonso tidzagawira timapepala toitanira anthu kumsonkhano wachigawo patatsala milungu itatu msonkhanowu usanachitike. Mipingo idzayesetse kugawira timapepalati m’gawo lonse la mpingo wawo ngati n’zotheka. (Onani bokosi lakuti “Kodi Tidzagawira Bwanji Timapepalati?”) Mudzatenge timapepala tonse totsala popita kumsonkhano wachigawo. Abale ndi alongo adzagwiritsira ntchito timapepalati polalikira anthu amene azidzakumana nawo m’dera limene kudzachitikire msonkhanowo.

9. Tchulani zitsanzo zosonyeza kuti anthu amabwera tikawaitanira kumsonkhano.

9 Kodi anthu amapitadi kumsonkhano wachigawo tikawaitana? Pamsonkhano wina wachigawo, kalinde wina anathandiza banja lina kupeza malo okhala. Iwo anafotokozera kalindeyo kuti analandira kapepala koitanira anthu kumsonkhano ndipo “anaona kuti msonkhanowu udzakhala wosangalatsa.” Choncho iwo anayenda mtunda wopitirira makilomita 320 kuti adzapezeke kumsonkhanowu. Komanso, mlongo wina ankagawira timapepalati kunyumba ndi nyumba. Atafika panyumba ina anagawira bambo wina yemwe ankaoneka kuti anali ndi chidwi ndi msonkhanowo. Choncho, iye anafotokozera bamboyu zambiri zokhudza msonkhanowu. Patangopita masiku ochepa, mlongoyu anaona bambo uja pamsonkhanowo ali ndi mnzake. Abambowa anali ndi mabuku amene anangotulutsidwa kumene pamsonkhanowo.

10. N’chifukwa chiyani kupezeka pamsonkhano wachigawo n’kofunika kwambiri?

10 Zikondwerero zapachaka zinkasonyeza chikondi chimene Yehova anali nacho pothandiza Aisiraeli “kum’tumikira mosalakwitsa ndiponso mokhulupirika.” (Yos. 24:14) Mofanana ndi Isiraeli, kuchita nawo misonkhano yathu yachigawo imeneyi kumatithandiza ‘kupitirizabe kuyenda m’choonadi’ ndipo kuchita zimenezi n’kofunika kwambiri pa kulambira kwathu. (3 Yoh. 3) Yehova apitirize kudalitsa zonse zimene anthu okonda choonadi akuchita kuti adzapezeke nawo pamisonkhanoyi kuti adzapindule mokwanira.

[Bokosi patsamba 3]

Gulu la Yehova lakonza msonkhano umene ndi wothandiza kwambiri pothana ndi mavuto amene anthu padziko lonse akukumana nawo

[Bokosi patsamba 4]

Makhalidwe athu abwino pamene tili kudera kumene kukuchitikira msonkhano amakometsera choonadi

[Bokosi patsamba 5]

Tidzagawira timapepala toitanira anthu kumsonkhano wachigawo patatsala milungu itatu msonkhanowu usanachitike

[Bokosi pamasamba 3-6]

Zofunika Kukumbukira pa Msonkhano Wachigawo

◼ Nthawi ya Msonkhano: Masiku onse atatu msonkhano uzidzayamba nthawi ya 8:20 m’mawa. Patangotsala mphindi zochepa kuti msonkhano uyambe tcheyamani azidzakhala pampando kupulatifomu ndipo nyimbo zamalimba zizidzayamba kuyimba. Tonse tiyenera kukhala pansi pa nthawi imeneyo kuti msonkhano uyambe bwinobwino. Tsiku loyamba ndi lachiwiri msonkhano udzatha 3:55 madzulo. Tsiku lachitatu, msonkhano udzatha nthawi ya 2:45 madzulo.

◼ Koimika Magalimoto: Malo onse ochitira msonkhano adzakhala ndi malo okwanira oimikako magalimoto ndi njinga. Tikukulimbikitsani kudzamvera zimene akalinde amene aikidwa kusamalira utumiki umenewu angakuuzeni. Eniake a magalimoto adzaonetsetse kuti zitseko za magalimoto ndi zokiya. Nawonso eniake a njinga adzaonetsetse kuti njinga zawo ndi zokhoma, asanakakhale pansi.

◼ Kusungirana Malo: Tingasungire malo anthu okhawo amene tabwera nawo pa galimoto imodzi kapena amene timakhala nawo nyumba imodzi komanso anthu amene panopa tikuphunzira nawo Baibulo.—1 Akor. 13:5.

◼ Chakudya Chamasana: Tikulimbikitsidwa kuti tidzabwere ndi chakudya chamasana, m’malo mochoka pamalo a msonkhano kukagula chakudya pa nthawi yopuma. Mungatenge zakudya zimene ena amakonda kutenga akakhala ndi zochitika zapadera monga tchipisi, mpunga wophika, mbatata, chinangwa ndi zakumwa. Koma mowa si wololedwa pamalo a msonkhano.

◼ Zopereka: Tingasonyeze kuyamikira ntchito yomwe inagwiridwa pokonzekera msonkhanowu popereka mwaufulu ndalama zothandiza pa ntchito ya padziko lonse. Tingapereke ndalamazi ku Nyumba ya Ufumu yathu kapena pamsonkhanopo. Polemba macheke operekedwa pamsonkhano wachigawo, sonyezani kuti ndalamazo zikupita ku “Watch Tower Society.”

◼ Ngozi Ndiponso Matenda Adzidzidzi: Ngati munthu wadwala mwadzidzidzi pamsonkhanopo, dziwitsani kalinde amene ali pafupi, ndipo iye mwamsanga adzadziwitsa a Dipatimenti ya Zachipatala kuti anthu odziwa bwino zachipatala amene alipo adzaone mmene zinthu zilili ndiponso thandizo limene angapereke.

◼ Ovutika Kumva: Nkhani za msonkhanowu adzazimasulira m’Chinenero cha Manja, kumsonkhano wachigawo wa Chingelezi wa ku Lilongwe, Blantyre ndi malo ena. Zimenezi zidzalengezedwa pa tsiku loyamba la msonkhanowo m’chigawo choyamba.

◼ Kujambula Mawu: Musadzalumikize zipangizo zanu zojambulira ku magetsi kapena kuzokuzira mawu za pamsonkhano ndipo mudzasamale kuti zisasokoneze ena.

◼ Mafomu a Kaonaneni ndi Wachidwi Uyu: Pofotokoza za munthu aliyense amene anaonetsa chidwi mutamulalikira mwamwayi pa nthawi ya msonkhano, muzigwiritsa ntchito mafomu a Kaonaneni ndi Wachidwi Uyu (S-43). Ofalitsa adzabweretse fomu imodzi kapena awiri kumsonkhano. Mungapereke mafomu osainidwa bwinobwino ku Chipinda cha Mabuku kapena kwa mlembi wa mpingo wanu mukabwerako kumsonkhanowo.—Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 2009, tsa. 4 ndime 5 ndi 6.

◼ Kujambula Zithunzi: Ngati mukujambula zithunzi, musagwiritse ntchito fulashi msonkhano uli mkati.

◼ Mafoni a M’manja: Muyenera kuwazimitsa kapena kuwatchera m’njira yoti asasokoneze anthu.

◼ Utumiki Wodzipereka: Timasangalala kwambiri ndi msonkhano wachigawo tikadzipereka kuchita nawo utumiki mwa kufuna kwathu. (Mac. 20:35) Ngati mukufuna kuchita nawo utumikiwu, kaonaneni ndi abale a ku Dipatimenti ya Antchito Odzipereka. Ana osafika zaka 16 angachite nawo utumiki umenewu moyang’aniridwa ndi makolo awo kapena munthu wina wachikulire wovomerezedwa ndi makolowo.

[Bokosi patsamba 6]

Kodi Tidzagawira Bwanji Timapepalati?

Kuti tidzagawire timapepalati m’gawo lathu lonse, ndi bwino kulankhula mwachidule. Mwina tinganene kuti: “Takupezani. Tikugwira ntchito imene ikuchitika padziko lonse yogawira timapepala iti toitanira anthu kumsonkhano. Landirani kapepala kanu. Zonse zokhudza msonkhanowu zili pakapepala kameneka.” Mukhale ndi nsangala. Ngati mukugwira ntchito yogawira timapepalati kumapeto kwa mlungu, mungagawirenso magazini kwa munthu amene wachita chidwi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena