Masiku Atatu Otsitsimulidwa Mwauzimu
1. Kodi tiyembekezere kukalandira chiyani kumsonkhano wachigawo chaka chino?
1 M’dziko la Satana ndiponso louma mwauzimuli, Yehova akupitirizabe kutsitsimula atumiki ake. (Yes. 58:11) Njira imodzi imene Yehova akugwiritsa ntchito kuti atipatse mphamvu ndiyo msonkhano wachigawo. Pamene msonkhano wachigawo wa chaka chino ukuyandikira, kodi tingakonzekere bwanji kukatsitsimulidwa ndiponso kukatsitsimula ena?—Miy. 21:5.
2. Kodi tiyenera kukonzekera zinthu ziti?
2 Ngati simunayambe kukonzekera, yambani panopo kukonzekera ndiponso kudziwitsa abwana anu, kuti mudzapezeke masiku onse atatu a msonkhano wachigawowu. Kodi mwadziwa kale nthawi imene muyenera kunyamuka popita kumalo a msonkhano tsiku ndi tsiku kuti muzikafika nthawi yabwino ndiponso kupeza malo okhala pulogalamu isanayambe? Sitikufuna kudzaphonya mbali iliyonse ya chakudya chauzimu chopatsa mphamvu chimene Yehova watikonzerachi. (Yes. 65:13, 14) Kodi mwakonzeratu za malo ogona ndiponso za mmene muzidzayendera?
3. Tchulani mfundo zimene inuyo ndi banja lanu mungatsatire kuti mudzapindule ndi msonkhano wachigawo.
3 Kodi mungachite chiyani kuti maganizo anu asamadzayendeyende pulogalamu ili mkati? Ngati zingatheke, muzidzagona mokwanira masiku onse a msonkhano wachigawo. Muzidzayang’ana wokamba nkhani ndiponso muzidzatsegula lemba lililonse limene latchulidwa m’Baibulo lanu komanso kulemba notsi. Zingakhale bwinonso kuti banja lonse lizidzakhala pamodzi kuti makolo adzathandize ana awo kumvetsera msonkhanowu mwachidwi. (Miy. 29:15) Mungachite bwinonso kuti madzulo aliwonse muzidzakambirana mfundo zikuluzikulu zimene mwapeza ku msonkhanowu. Kuti banja lanu lidzapitirize kukhala lotsitsimulidwa msonkhanowu ukatha, pa nthawi ya Kulambira kwa pabanja muzidzapatula nthawi yokambirana mfundo zimene mungazitsatire.
4. Kodi tingathandize bwanji ena mu mpingo kuti adzatsitsimulidwe mwauzimu?
4 Thandizani Ena Kuti Akatsitsimulidwe: Tikufuna kuti anthu enanso adzatsitsimulidwe mwauzimu. Kodi mu mpingo wanu muli ofalitsa achikulire kapena ena amene akufunikira thandizo kuti akafike kumsonkhano wachigawo? Kodi inuyo mungathandizepo? (1 Yoh. 3:17, 18) Akulu, makamaka oyang’anira timagulu, aonetsetse kuti ofalitsa oterewa alandira thandizo limene akufunikira.
5. Kodi tidzagawira bwanji timapepala toitanira anthu kumsonkhano wachigawo? (Onaninso bokosi limene lili patsamba 5.)
5 Monga mmene takhala tikuchitira m’mbuyomu, kutatsala milungu itatu kuti msonkhano wachigawo uyambe, tidzagwira ntchito yogawira timapepala toitanira anthu kumsonkhano wachigawo. Mipingo iyenera kukhala ndi cholinga chogawira timapepala tonse timene yalandira m’dera lalikulu mmene ingathere.
6. Tchulani njira zimene tingasonyezere khalidwe labwino pamsonkhano wachigawo.
6 Khalidwe Labwino Limatsitsimula: Pa nthawi imene anthu ambiri ndi “odzikonda” ndipo amachita zinthu mosaganizira ena, zimakhala zotsitsimula kukhala pakati pa Akhristu anzathu amene akuyesetsa kukhala ndi khalidwe labwino. (2 Tim. 3:2) Timasonyeza khalidwe labwino tikamalowa mosapanikizana ndiponso mwadongosolo pamalo a msonkhano, kusungira malo anthu a m’banja lathu okha, amene tayenda nawo pa galimoto imodzi ndiponso amene tikuphunzira nawo Baibulo. Timasonyezanso khalidweli tikamamvera tcheyamani pamene watipempha kukhala pansi kuti timvere nyimbo zamalimba chigawo chilichonse cha msonkhano chikamayamba. Tingasonyezenso khalidweli ngati titatchera foni yathu m’njira yoti isasokoneze ena nthawi ya pulogalamu, ndiponso kupewa kulankhulana, kutumiza mauthenga a pafoni, kudya kapenanso kuyendayenda msonkhano uli mkati.
7. Kodi tingatani kuti tidzatsitsimulidwe kapena kutsitsimula abale athu pamsonkhano?
7 Kucheza Kotsitsimula: Misonkhano yachigawo imatipatsa mwayi wocheza ndiponso kulimbikitsana ndi abale achikhristu. (Sal. 133:1-3) Mungachite bwino ‘kudzafutukula mtima wanu’ kuti mudzadziwane ndi abale ndi alongo amene abwera kuchokera kumipingo ina. (2 Akor. 6:13) Mungakhalenso ndi cholinga chodziwana ndi munthu mmodzi kapena banja lina tsiku lililonse. Mungachite zimenezi nthawi ya chakudya chamasana. Choncho, kuti mudzakwanitsedi kuchita zimenezi, mudzatenge chakudya choti mukadyere kumsonkhano m’malo mopita kukagula kapena kukadya kulesitilanti. Zimenezi zidzakuthandizani kupeza mabwenzi atsopano ndiponso amene mudzakhala nawo mpaka kalekale.
8. N’chifukwa chiyani tiyenera kudzipereka kukagwira ntchito kumsonkhano wachigawo ndipo tingachite bwanji zimenezi?
8 Zimakhalatu zotsitsimula kuchita utumiki wopatulika limodzi ndi olambira anzathu. Kodi inuyo mungadzipereke kukathandiza m’dipatimenti inayake kapena mungathandize mpingo wanu pa ntchito yoyeretsa malo a msonkhano imene wapatsidwa? (Sal. 110:3) Ngati panopa mulibe zochita, tikukupemphani kuti mukalembetse ku Dipatimenti ya Antchito Odzipereka kumsonkhano wachigawo. Pakachuluka ogwira ntchito, ntchitoyo imasangalatsa ndiponso imapepuka.
9. N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala kwambiri ndi khalidwe ndiponso kaonekedwe kathu nthawi ya msonkhano wachigawo?
9 Khalidwe Lathu Limatsitsimula Anthu Otiona: Timakhala tili pamsonkhano masiku onse atatu a msonkhano wachigawo, osati nthawi ya pulogalamu yokhayo. Anthu amene amationa kumzinda kapena dera limene kukuchitikira msonkhano azitha kusiyanitsa Mboni ndi anthu amene si Mboni. (1 Pet. 2:12) Nthawi zonse, zovala ndi kudzikongoletsa kwathu pamene tili pamalo a msonkhano, kumene tikugona ndiponso pamene tikudya kulesitilanti zizilemekeza Yehova. (1 Tim. 2:9, 10) Ngati titavala baji yathu, anthu otiona adzatizindikira kuti ndife Mboni za Yehova. Zimenezi zingatipatse mwayi wowauza za msonkhano wathu ndiponso kuwalalikira.
10. Fotokozani zokumana nazo zimene zimapereka umboni wabwino chifukwa cha khalidwe labwino lachikhristu.
10 Kodi anthu ena amakhala ndi chithunzi chotani akaona khalidwe lathu labwino nthawi ya msonkhano wachigawo? Malinga ndi zimene nyuzipepala ina inalemba, manijala wa malo ena amene kunachitikira msonkhano wachigawo anati: “Anthu ake ndi aulemu. Timasangalala kuwapatsa malo chaka chilichonse.” Chaka chatha, munthu wina amene si Mboni anataya kachikwama kake kandalama kuhotela imene kunkagona abale amene anapita kumsonkhano wachigawo. Manijala wa hotelayi atalandira kachikwamaka zinthu zonse zili momwemo, anauza mwiniwake wa kachikwamako kuti: “Uli ndi mwayi kuti Mboni za Yehova zinali kuchita msonkhano cha kufupi ndi kuno, ndipo ambiri anali kugona pahotela ino. Akanakhala anthu ena sakanabweza kachikwama kandalamaka.”
11. Pamene msonkhano wachigawo ukuyandikira, kodi tiyenera kukhala ndi cholinga chotani ndipo chifukwa chiyani?
11 Misonkhano yachigawo yayandikira kwambiri. Abale atherapo nthawi ndiponso achita khama kwambiri kukonza pulogalamu komanso malo a msonkhano kuti adzakhale osangalatsa. Khalani ndi cholinga choti mudzapezeke masiku onse atatu ndipo konzekerani kudzalandira malangizo amene Yehova ndi gulu lake akukonzerani. Konzekerani kudzakhala otsitsimula kwa ena chifukwa cha khalidwe lanu ndiponso kucheza momasuka. Mukatero, inuyo ndiponso ena mudzamva ngati mmene munthu wina amene anapezeka pamsonkhanowu chaka chatha anamvera. Iye analemba kuti: “Sindikukumbukiranso msonkhano wina wosangalatsa kuposa msonkhano umenewu.”
[Mawu Otsindika patsamba 3]
Monga mmene takhala tikuchitira m’mbuyomu, kutatsala milungu itatu kuti msonkhano wachigawo uyambe, tidzagwira ntchito yogawira timapepala toitanira anthu kumsonkhano wachigawo
[Mawu Otsindika patsamba 4]
Nthawi zonse, zovala ndi kudzikongoletsa kwathu pamene tili pamalo a msonkhano, kumene tikugona ndiponso pamene tikudya kulesitilanti zizilemekeza Yehova
Konzekerani kudzakhala otsitsimula kwa ena chifukwa cha khalidwe lanu ndiponso kucheza momasuka
[Bokosi patsamba 5]
Zofunika Kukumbukira pa Msonkhano Wachigawo
◼ Nthawi ya Mapulogalamu: Masiku onse atatu msonkhano uzidzayamba nthawi ya 8:20 m’mawa. Patangotsala mphindi zochepa kuti msonkhano uyambe tcheyamani adzakhala pampando kupulatifomu ndipo nyimbo zamalimba zidzayamba kuyimba. Tonse tiyenera kukhala pansi pa nthawi imeneyo kuti msonkhano uyambe bwinobwino. Tsiku loyamba ndi lachiwiri, msonkhano uzidzatha nthawi ya 4:05 madzulo, ndipo tsiku lomaliza udzatha nthawi ya 2:50 madzulo.
◼ Koimika Magalimoto: Malo onse ochitira msonkhano adzakhala ndi malo okwanira oimikako magalimoto ndi njinga. Tikukulimbikitsani kudzamvera zimene akalinde amene aikidwa kusamalira utumiki umenewu angakuuzeni. Eniake a magalimoto adzaonetsetse kuti zitseko za magalimoto ndi zokiya, ndipo nawonso eniake a njinga adzaonetsetse kuti njinga zawo ndi zokhoma, asanakakhale pansi.
◼ Kusungirana Malo: Tingasungire malo anthu okhawo amene tabwera nawo pa galimoto imodzi kapena amene timakhala nawo nyumba imodzi komanso anthu amene panopa tikuphunzira nawo Baibulo.—1 Akor. 13:5.
◼ Chakudya Chamasana: Tikulimbikitsidwa kuti tidzabwere ndi chakudya chamasana, m’malo mochoka pamalo a msonkhano kukagula chakudya pa nthawi yopuma. Mungatenge zakudya zimene ena amakonda kutenga akakhala ndi zochitika zapadera monga tchipisi, mpunga wophika, mbatata, chinangwa ndi zakumwa. Koma mowa si wololedwa pamalo a msonkhano.
◼ Zopereka: Tingasonyeze kuyamikira ntchito yomwe inagwiridwa pokonzekera msonkhanowu popereka mwaufulu ndalama zothandiza pa ntchito ya padziko lonse. Tingapereke ndalamazi ku Nyumba ya Ufumu yathu kapena pamsonkhanopo. Polemba macheke operekedwa pa msonkhano wachigawo, sonyezani kuti ndalamazo zikupita ku “Watch Tower Society.”
◼ Ngozi Ndiponso Matenda Adzidzidzi: Ngati munthu wadwala mwadzidzidzi pamsonkhanopo, dziwitsani kalinde amene ali pafupi, ndipo iye mwamsanga adzadziwitsa a Dipatimenti ya Zachipatala kuti anthu odziwa bwino zachipatala amene alipo adzathe kuona mmene zinthu zilili ndiponso thandizo limene angapereke.
◼ Ovutika Kumva: Nkhani za msonkhanowu adzazimasulira m’Chinenero cha Manja, ku msonkhano wachigawo wa Chingelezi wa ku Lilongwe, Blantyre ndi malo ena. Zimenezi zidzalengezedwa pa tsiku loyamba la msonkhanowo m’chigawo choyamba.
◼ Kujambula Mawu: Zipangizo zanu zojambulira musazilumikize ku magetsi kapena kuzokuzira mawu za pamsonkhano ndipo muyenera kudzazigwiritsa ntchito m’njira yoti zisasokoneze ena.
◼ Mafomu a Kaonaneni ndi Wachidwi Uyu: Pofotokoza za munthu aliyense amene anaonetsa chidwi mutamulalikira mwamwayi pa nthawi ya msonkhano, muzigwiritsa ntchito mafomu a Kaonaneni ndi Wachidwi Uyu (S-43). Ofalitsa azibweretsa fomu imodzi kapena awiri kumsonkhano. Mungapereke mafomu osainidwa bwinobwino ku Chipinda cha Mabuku kapena kwa mlembi wa mpingo wanu mukabwerako kumsonkhanowo.—Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 2009, tsa. 4.
◼ Kujambula Zithunzi: Ngati mukujambula zithunzi, musagwiritse ntchito fulashi msonkhano uli mkati.
◼ Mafoni a M’manja: Muyenera kuwazimitsa kapena kuwatchera m’njira yoti asasokoneze anthu.
◼ Utumiki Wodzipereka: Timasangalala kwambiri ndi msonkhano wachigawo tikadzipereka kuchita nawo utumiki mwa kufuna kwathu. (Mac. 20:35) Ngati mukufuna kuchita nawo utumikiwu, kaonaneni ndi abale a ku Dipatimenti ya Antchito Odzipereka. Ana osafika zaka 16 angachite nawo utumiki umenewu moyang’aniridwa ndi makolo awo kapena munthu wina wachikulire wovomerezedwa ndi makolowo.
[Bokosi patsamba 5]
Kodi Tidzagawira Bwanji Timapepalati?
Kuti tidzagawire timapepalati m’gawo lathu lonse, ndi bwino kulankhula mwachidule. Mwina tingenene kuti: “Takupezani. Tikugwira ntchito imene ikuchitika padziko lonse yogawira timapepala iti toitanira anthu kumsonkhano. Landirani kapepala kanu. Zonse zokhudza msonkhanowu zili pakapepala kameneka.” Zimene zili patsogolo pa kapepalaka ndi zochititsa chidwi, choncho m’patseni mwininyumbayo kuti aone. Mukhale ndi nsangala. Ngati mukugwira ntchito yogawira timapepalati kumapeto kwa mlungu, mungagawirenso magazini kwa munthu amene wasonyeza chidwi.