Misonkhano Yachigawo Ndi Nthawi Imene Timalambira Mulungu Mosangalala
1. Kodi misonkhano yachigawo imene timachita masiku ano ndi yofanana bwanji ndi zikondwerero zimene Aisiraeli anali kuchita?
1 Nthawi zonse Yosefe, Mariya, ndi ana awo ndiponso anthu ena ankapita ku Yerusalemu ku zikondwerero zapachaka. Panthawi ya zikondwererozi, iwo ndi anthu ena olambira Yehova anali kusiya ntchito zawo kuti achite zinthu zauzimu zofunika kwambiri pa moyo wawo. Zikondwerero zapachaka zimenezi zinali kuwapatsa mpata woganizira ndiponso kukambirana madalitso amene Yehova anawapatsa komanso mfundo za m’Chilamulo. Misonkhano yachigawo imene ikubwerayi idzatipatsanso mwayi ngati umenewu wolambira Yehova mosangalala.
2. Kodi tingachite chiyani pokonzekera msonkhano wachigawo umene ukubwerawu?
2 Tifunika Kukonzekera: Pa ulendo wochoka ku Nazarete kupita ku Yerusalemu, Yesu, makolo, ndi abale ake anafunika kuyenda pansi ulendo wamakilomita pafupifupi 200, kupita ndi kubwera. Ngakhale kuti sitikudziwa kuti Yesu anali ndi abale ndi alongo angati, iyenera kuti inali ntchito yaikulu kwa Yosefe ndi Mariya kukonzekera ulendowu. Kodi inuyo mwakonzekera kudzapezeka pa msonkhano wachigawo masiku onse atatu? Kuti zimenezi zitheke mungafunike kutenga tchuthi kapena kupempha abwana anu kuti musadzabwere kuntchito nthawi imeneyi kapena kupemphanso aphunzitsi a mwana wanu kuti mwanayo amulole kudzapezeka pa msonkhano masiku amenewa. Ngati mungadzafune malo ogona, kodi mwakonza kale zimenezi? Kodi mungakonze zodzathandiza ena a mu mpingo wanu amene akufunika thandizo kuti adzathe kupezeka pa msonkhanowu?—1 Yoh. 3:17, 18.
3. Kodi zikondwerero zimene Ayuda anali kuchita zinali kupereka bwanji mpata wocheza ndi kulimbikitsana?
3 Kulimbikitsana: Zikondwerero za Ayuda zinali kuwapatsa mwayi wocheza ndiponso kulimbikitsana ndi olambira anzawo. N’zosakayikitsa kuti Yesu, makolo ndi abale ake anali kuyembekezera mwachidwi kukacheza ndi anzawo amene anaonana nawo kalekale. Iwo ayenera kuti anali kusangalala kupeza mabwenzi atsopano mwa Ayuda anzawo ndiponso anthu amene analowa chipembedzo chachiyuda, amene anakumana nawo pa zikondwererozo ku Yerusalemu ndiponso popita ndi pobwera.
4. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira ubale wathu wachikhristu?
4 Chifukwa china chimene kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amakonzera misonkhano yachigawo m’malo mongotilembera nkhanizo m’mabuku ndi chakuti tizicheza ndiponso kulimbikitsana ndi okhulupirira anzathu. (Aheb. 10:24, 25) Choncho, mukonzekere kudzafika mofulumira tsiku lililonse kuti mudzacheze ndi Akhristu anzanu, tcheyamani wachigawocho asananene kuti nyimbo zamalimba zikuyamba, zosonyeza kuti ndi nthawi yakuti tikhale pansi. M’malo mochoka pamalo amsonkhano nthawi ya masana kuti tikagule chakudya, ndi bwino kubweretsa chakudya chochepa kuti panthawi yamasana tidzakhalebe pamalo amsonkhano kuti tizicheza ndi anzathu. Ubale wathu wachikhristu ndi mphatso imene Yehova watipatsa ndipo ndi yofunika kuiyamikira.—Mika 2:12.
5. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tipindule kwambiri ndi msonkhano?
5 Nthawi Yophunzira: Kuyambira ali mwana, Yesu anali kupezerapo mwayi pa zikondwerero za ku Yerusalemu kuti aphunzire za Atate ake akumwamba. (Luka 2:41-49) Nanga n’chiyani chimene chingatithandize ifeyo ndiponso mabanja athu kuti tidzapindule ndi msonkhanowu? Mudzapewe kuyendayenda ndiponso kulankhulalankhula msonkhano uli mkati. Mudzaonetsetse kuti mafoni anu kapena zipangizo zina zisakusokonezeni komanso kusokoneza ena. Muzidzayang’ana wokamba nkhaniyo ndiponso kulemba notsi. Mudzakhale pamodzi ndi banja lanu ndipo mudzaonetsetse kuti ana anu akumvetsera. Mukaweruka, muzidzakambirana mfundo zimene zakusangalatsani.
6. Kodi tiyenera kukumbukira chiyani pa nkhani ya kavalidwe kathu ndiponso kudzikongoletsa?
6 Kavalidwe Ndiponso Kudzikongoletsa: Anthu amalonda a m’mayiko ena, amene anali kuyenda pamsewu wopita ku Yerusalemu, ayenera kuti anali kuzindikira Yesu, makolo ndi abale ake ndiponso Ayuda ena olambira Yehova akamapita ndiponso akamabwera ku msonkhano. Ayenera kuti anali kuwazindikira chifukwa zovala zawo zinali ndi mphonje zomwe zinali ndi kamzera ka buluu. (Num. 15:37-41) Ngakhale kuti Akhristu savala zovala zapadera, timadziwika chifukwa timavala mwaulemu ndiponso mwaukhondo. Tiyenera kuvala bwino makamaka popita ndiponso pochokera ku msonkhano komanso nthawi imene tili mumzinda umene mukuchitikira msonkhanowo. Pa masiku a msonkhano wachigawo, tikaweruka madzulo ndipo tasintha zovala, tionetsetse kuti tavalabe mwaulemu ndiponso tavala baji ya msonkhano. Ngati tichita zimenezi tidzakhala osiyana ndi anthu amene si Mboni za Yehova ndiponso tidzapereka chitsanzo chabwino kwa anthu otiona.
7. N’chifukwa chiyani tiyenera kukonzekera kudzagwira nawo ntchito pa msonkhano wachigawo?
7 Pakufunika Antchito Odzifunira: Kuti msonkhano uyende bwino pamafunika anthu ambiri kuti athandize pa ntchito zosiyanasiyana. Kodi mungadzathandize nawo pa ntchitozi? (Sal. 110:3) Ntchito imene imagwiridwa pa msonkhano ndi mbali ya utumiki wathu wopatulika ndipo ndi ulaliki pawokha. Mwachitsanzo bwana wa pamalo ena amene Mboni za Yehova zinachitira msonkhano wachigawo, anachita chidwi kwambiri ndi mmene Mbonizo zinasiyira malowo moti analemba kuti: “Ndikukuyamikirani kwambiri chifukwa chosamalira bwino malo ano kuposa anthu ena amene amadzachitira misonkhano yawo pamalo amenewa. Ndakhala ndikumva kuti Mboni za Yehova ndi anthu apadera kwambiri chifukwa amasiya malo amene achitira msonkhano ali ooneka bwino kuposa mmene anawapezera. Inuyo komanso gulu lanu lonse lasiya malo ano ali abwino kwambiri ndipo tikuona kuti tagwira ntchito ndi anthu aulemu kwambiri omwe sitinawaonepo chiyambire.”
8. Kodi tidzakhala ndi mipata yotani yolalikira m’dera limene tikuchitira msonkhano?
8 Mwayi Wolalikira: Anthu ambiri m’dera limene tikuchitira msonkhano amachita chidwi tikavala komanso kudzikongoletsa moyenera ndiponso tikavala mabaji. Zimenezi zingachititse kuti iwo afune kudziwa chifukwa chake tavala choncho ndipo umenewu ungakhale mwayi wowafotokozera zambiri zokhudza msonkhanowo. Mwachitsanzo, madzulo atachoka ku msonkhano, mwana wina wazaka zinayi popita kulesitilanti anatenga buku lomwe linali litatuluka ku msonkhanowo ndipo anaonetsa bukulo mayi wina woperekera zakudya. Zimenezi zinathandiza kuti makolo a mwanayo aitanire mayiyo ku msonkhanowo.
9. Kodi tingatsatire bwanji zimene Yesu, makolo, ndi abale ake anali kuchita poyamikira zinthu zauzimu zochokera kwa Yehova?
9 Zikondwerero za ku Yerusalemu zinali zosangalatsa ndipo Ayuda okonda zinthu zauzimu anali kuziyembekezera mwachidwi. (Deut. 16:15) Yesu, makolo, ndi abale ake anali kusangalala ndi zikondwererozi ndipo anali kulolera kudzimana zinthu zina kuti akapezeke komanso akapindule ndi zikondwererozo. Nafenso timasangalala kwambiri ndi misonkhano yachigawo ndipo timaiona kuti ndi mphatso yochokera kwa Atate wathu wakumwamba. (Yak. 1:17) Panopo tiyenera kuyamba kukonzekera kudzapezeka ku msonkhano wachigawo kuti tikalambire Yehova mosangalala.
[Bokosi patsamba 6]
Zofunika Kukumbukira pa Msonkhano Wachigawo
◼ Nthawi ya Mapulogalamu: Kwa masiku onse atatu msonkhano uzidzayamba nthawi ya 8:20 m’mawa. Patangotsala mphindi zochepa kuti msonkhano uyambe tcheyamani adzakhala pampando kupulatifomu ndipo nyimbo zamalimba zidzayamba kuyimba. Tonse tiyenera kukhala pansi panthawi imeneyo kuti msonkhano uyambe bwinobwino. Tsiku loyamba, msonkhano udzatha nthawi ya 4:25 madzulo, tsiku lachiwiri udzatha 3:55 madzulo ndipo tsiku lomaliza udzatha nthawi ya 2:40 madzulo.
◼ Koimika Galimoto: Malo onse ochitira msonkhano adzakhala ndi malo okwanira oimikako magalimoto ndi njinga. Tikukulimbikitsani kudzamvera zimene akalinde amene aikidwa kusamalira utumiki umenewu angakuuzeni. Eniake a magalimoto afunikira kudzaonetsetsa kuti zitseko za magalimoto ndi zokiya, ndipo nawonso eniake a njinga adzaonetsetse kuti njinga zawo ndi zokhoma, asanakakhale pansi.
◼ Kusungirana Malo: Tingasungire malo anthu okhawo amene tabwera nawo pa galimoto imodzi kapena amene timakhala nawo nyumba imodzi komanso anthu amene panopa tikuphunzira nawo Baibulo.—1 Akor. 13:5.
◼ Chakudya Chamasana: Tikulimbikitsidwa kuti tidzabwere ndi chakudya chamasana, m’malo mochoka pamalo a msonkhano kukagula chakudya panthawi yopuma. Mungatenge zakudya zimene ena amakonda kutenga akakhala ndi zochitika zapadera monga tchipisi, mpunga wophika, mbatata, chinangwa ndi zakumwa. Koma mowa si wololedwa pamalo a msonkhano
◼ Zopereka: Tingasonyeze kuyamikira ntchito yomwe inagwiridwa pokonzekera msonkhanowu mwa kupereka mwaufulu ndalama zothandiza pa ntchito ya pa dziko lonse. Tingapereke ndalamazi ku Nyumba ya Ufumu yathu kapena pamsonkhanopo. Polemba macheke operekedwa pa msonkhano wachigawo, sonyezani kuti ndalamazo zikupita ku “Watch Tower Society.”
◼ Ngozi Ndiponso Matenda Amwadzidzidzi: Ngati munthu wadwala mwadzidzidzi pamsonkhanopo, dziwitsani kalinde amene ali pafupi, ndipo iye mwamsanga adzadziwitsa a Dipatimenti ya Zachipatala kuti anthu odziwa bwino zachipatala amene alipo adzathe kuona mmene zinthu zilili ndiponso thandizo limene angapereke.
◼ Ovutika Kumva: Nkhani za msonkhanowu adzazimasulira m’Chinenero cha Manja, ku msonkhano wachigawo wa Chingelezi wa ku Blantyre, Lilongwe ndi ku Mzuzu. Zimenezi zidzalengezedwa pa tsiku loyamba la msonkhanowo m’chigawo choyamba.
◼ Kujambula Mawu: Zipangizo zanu zojambulira musazilumikize ku magetsi kapena kuzokuzira mawu za pa msonkhano ndipo muyenera kudzazigwiritsa ntchito m’njira yoti zisasokoneze ena.
◼ Mafomu Odziwitsira Ena za Munthu Wachidwi: Pofotokoza za munthu aliyense amene anaonetsa chidwi mutamulalikira mwamwayi panthawi ya msonkhano, gwiritsani ntchito mafomu a Kaonaneni ndi Wachidwi Uyu (S-43). Ofalitsa azibweretsa fomu imodzi kapena awiri ku msonkhano. Mungapereke mafomu osainidwa bwinobwino ku Chipinda cha Mabuku kapena kwa mlembi wa mpingo wanu mukabwerako ku msonkhanowo.—Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 2009, tsamba 4.
◼ Kujambula Zithunzi: Ngati mukujambula zithunzi, musagwiritse ntchito fulashi msonkhano uli mkati.
◼ Mafoni a M’manja: Muyenera kuthimitsa kapena kuwatchera kuti asalire n’kusokoneza ena.
◼ Utumiki Wodzifunira: Timasangalala kwambiri ndi msonkhano wachigawo tikadzipereka kuchita nawo utumiki wodzifunira. (Mac. 20:35) Ngati mukufuna kuchita nawo utumikiwu, kaonaneni ndi abale a ku Dipatimenti ya Utumiki Wodzifunira. Ana osafika zaka 16 angachite nawo utumiki umenewu ngati angamagwire moyang’aniridwa ndi makolo awo kapena munthu wina wachikulire wovomerezedwa ndi makolowo.