Ndandanda ya Mlungu wa June 25
MLUNGU WOYAMBIRA JUNE 25
Nyimbo Na. 39 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 8 ndime 1-7 ndi mabokosi patsamba 61 ndi 62 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Ezekieli 1-5 (Mph. 10)
Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu (Mph. 20)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zilengezo. Pogwiritsa ntchito chitsanzo cha ulaliki chimene chili patsamba 8, chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingagwiritsire ntchito magaziniwa poyambitsa phunziro la Baibulo Loweruka loyambirira m’mwezi wa July.
Mph. 15: Gwiritsirani Ntchito Nthawi Yanu Mwanzeru Pamene Muli mu Utumiki. (Aef. 5:15, 16) Nkhani yokambirana pogwiritsa ntchito mafunso awa: (1) Kodi tingagwiritsire ntchito bwanji nthawi yathu mwanzeru pamene: (a) tikuchititsa msonkhano wokonzekera kulowa mu utumiki wakumunda? (b) msonkhano wokonzekera kulowa mu utumiki wakumunda ukatha? (c) wofalitsa wina m’gulu lathu akukambirana ndi munthu wachidwi kwa nthawi yaitali? (d) tili ndi maulendo obwereza amene sakhala moyandikana? (2) Kodi tingapewe bwanji kuwononga nthawi ngati: (a) banja lathu ladyeratu chakudya tisanapite kumsonkhano wokonzekera kulowa mu utumiki wakumunda? (b) aliyense angafike mwamsanga pamsonkhano wokonzekera kulowa mu utumiki wakumunda? (c) tamvetsera mwatcheru pamene akutigawira munthu woti tilowe naye mu utumiki kuti wotsogolera mu utumiki asatigawenso pambuyo pa pemphero la msonkhanowo? (d) aliyense akudziwa gawo limene akukalalikira asananyamuke?
Mph. 10: Zimene Munganene Pogawira Magazini M’mwezi wa July. Nkhani yokambirana. Sankhani mitu iwiri kapena itatu ndipo mufotokoze kwa mphindi yosapitirira imodzi mmene mitu imeneyi ingakhalire yogwira mtima kwa anthu a m’gawo lanu. Kenako, pogwiritsa ntchito nkhani zoyambirira za mu Nsanja ya Olonda, pemphani omvera kuti afotokoze mafunso amene angakope chidwi cha anthu ndiponso malemba amene angawerenge. Chitaninso chimodzimodzi ndi nkhani zoyambirira za mu Galamukani! Ngati nthawi ilipo chitaninso chimodzimodzi ndi nkhani zina za m’magaziniwa. Chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungagawirire magazini iliyonse.
Nyimbo Na. 29 ndi Pemphero