Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa tidzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira June 25, 2012. Taika tsiku limene likusonyeza mlungu umene mfundoyo ikuyenera kukambidwa n’cholinga choti muthe kufufuza pamene mukukonzekera sukulu mlungu uliwonse.
1. Kodi tingaphunzire chiyani poona mmene Yeremiya anapulumukira pa nthawi imene panali mavuto a zachuma? (Yer. 37:21) [May 7, w97 9/15 tsa. 3 ndime 4–tsa. 4 ndime 1]
2. Kodi Akhristu amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi amatsanzira bwanji chitsanzo chabwino cha Ebedi-meleki? (Yer. 38:8-13) [May 7, su tsa. 179 ndime 9]
3. Popeza Yehova anagwiritsa ntchito asilikali a Nebukadirezara kuti ateteze Yeremiya ndi Baruki, kodi n’koyenera kuti Akhristu azipempha chitetezo cha apolisi masiku ano? (Yer. 39:11-14) [May 14, w83-E 7/15 tsa. 31; lv tsa. 44 ndime 18]
4. Kodi “zinthu zazikulu” zimene Baruki ankafuna zinali chiyani ndipo tingaphunzire chiyani pa zimene anachita atapatsidwa uphungu ndi Yehova? (Yer. 45:5) [May 21, w06 8/15 tsa. 18 ndime 1; tsa. 19 ndime 6]
5. N’chifukwa chiyani Yehova anadziyerekezera ndi “okolola mphesa” ndiponso “akuba” pamene ankafotokoza za chiweruzo chimene chinali kubwera pa dziko la Edomu? (Yer. 49:9, 10) [May 28, w07 11/1 tsa. 13 ndime 4; w77-E tsa. 442 ndime 7–tsa. 443 ndime 1]
6. Kodi tingaphunzire mfundo zochititsa chidwi ziti poona zimene zinachitikira Mfumu Zedekiya ‘atapandukira mfumu ya Babulo’? (Yer. 52:3, 7-11) [June 4, w88 9/15 tsa. 17 ndime 8; w81-E 4/1 tsa. 13 ndime 3-4; tsa. 14 ndime 6]
7. Kodi “chopondapo mapazi” ndiponso “chisimba” cha Yehova n’chiyani? (Maliro 2:1, 6) [June 11, w07 6/1 tsa. 9 ndime 2]
8. Kodi Yeremiya ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti Yehova ‘adzakumbukira ndi kumuweramira,’ ndipo zimenezi n’zofunika kwambiri kwa ife chifukwa chiyani? (Maliro 3:20) [June 18, w07 6/1 tsa. 11 ndime 3]
9. N’chifukwa chiyani n’zothandiza kuti munthu aziphunzira kunyamula goli la mavuto ali mnyamata? (Maliro 3:27) [June 18, w07 6/1 tsa. 11 ndime 5; w87-E 2/15 tsa. 24 ndime 1]
10. Kodi chitsanzo cha Ezekieli chingatithandize bwanji kulankhula molimba mtima ngakhale pamene anthu sakulabadira? (Ezek. 3:8, 9) [June 25, w08 7/15 mas. 8-9 ndime 6-7]