Ndandanda ya Mlungu wa July 2
MLUNGU WOYAMBIRA JULY 2
Nyimbo Na. 54 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 8 ndime 8-16 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Ezekieli 6-10 (Mph. 10)
Na. 1: Ezekieli 7:14-27 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: N’chifukwa Chiyani Yonatani Ali Chitsanzo Chabwino Kwambiri pa Nkhani ya Kudzichepetsa?—1 Sam. 23:16-18 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi N’zoona Kuti Mkate ndi Vinyo Zimasandulika Kukhala Thupi ndi Magazi a Khristu?—rs tsa. 280 ndime 2–tsa. 282 ndime 1 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 3: Zilengezo.
Mph. 8: Kukambirana Ndi Anthu mu Utumiki—Mbali Yoyamba. Kukambirana ndi omvera mfundo zimene zikupezeka m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 251 mpaka tsamba 253, ndime 1. Chitani chitsanzo chachidule chosonyeza mmene tingagwiritsire ntchito mfundo imodzi kapena ziwiri za m’nkhaniyi.
Mph. 24: “Misonkhano Yathu Yachigawo Imafotokoza Mfundo za Choonadi.” Mafunso ndi mayankho. Kambiranani “Zofunika Kukumbukira pa Msonkhano Wachigawo.” Mukamakambirana ndime 8, funsani woyang’anira utumiki kuti afotokoze zimene zakonzedwa pa ntchito yogawira timapepala toitanira anthu kumsonkhano wachigawo.
Nyimbo Na. 119 ndi Pemphero