Yesetsani Kuti Muzisunga Nthawi
1. Kodi Yehova amatipatsa chitsanzo chotani pa nkhani ya kusunga nthawi?
1 Nthawi zonse, Yehova amasunga nthawi. Mwachitsanzo, iye amathandiza atumiki ake ‘pa nthawi imene akufunikira thandizolo.’ (Aheb. 4:16) Amaperekanso “chakudya [chauzimu] pa nthawi yoyenera.” (Mat. 24:45) Choncho sitingakayikire kuti tsiku lake lidzafika ndithu ndipo ‘silidzachedwa.’ (Hab. 2:3) Anthufe timapindula kwambiri chifukwa choti Yehova amasunga nthawi. (Sal. 70:5) Koma chifukwa chotanganidwa komanso chifukwa choti ndife opanda ungwiro, nthawi zina anthufe zimativuta kusunga nthawi. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kumasunga nthawi?
2. Kodi tikamasunga nthawi zimalemekeza bwanji Yehova?
2 Masiku otsiriza ano anthu ambiri ndi odzikonda komanso osadziletsa ndipo zimenezi zimachititsa kuti asamasunge nthawi. (2 Tim. 3:1-3) Choncho Akhristu akamayesetsa kusunga nthawi yofikira kuntchito, kumisonkhano, akagwirizana ndi munthu kapena pa zinthu zina, anthu ena amaona ndipo amalemekeza Yehova. (2 Pet. 2:12) Kodi mumayesetsa kufika kuntchito pa nthawi yake, koma nthawi zambiri mumachedwa kufika pamisonkhano kapena pa zochitika zina zauzimu? Tikamayesetsa kufika nthawi yabwino pamisonkhano n’kuimba nawo nyimbo yoyamba, timasonyeza kuti tikufunitsitsa kutsanzira Atate wathu wakumwamba, yemwe amachita zinthu mwadongosolo.—1 Akor. 14:33, 40.
3. N’chifukwa chiyani tingati tikamasunga nthawi timasonyeza kuti timaganizira anzathu?
3 Tikamasunga nthawi timasonyezanso kuti timaganizira ena. (Afil. 2:3, 4) Mwachitsanzo, tikamafika nthawi yabwino kumisonkhano, kuphatikizapo msonkhano wokonzekera utumiki, timapewa kusokoneza Akhristu anzathu. Koma ngati tili ndi chizolowezi chochedwa, timasonyeza kuti timaona zoti ndife ofunika kwambiri kuposa Akhristu anzathuwo. Tikamasunga nthawi timasonyeza kuti ndife akhama komanso odalirika, ndipo anthu amakonda munthu amene ali ndi makhalidwe amenewa.
4. Ngati nthawi zonse timachedwa, kodi tingatani kuti tizisunga nthawi?
4 Ngati nthawi zonse mumachedwa, ganizirani zinthu zimene zimachititsa. Ndi bwinonso kudziwiratu zinthu zimene mukufuna kuchita ndipo onetsetsani kuti mwazichita pa nthawi yake. (Mlal. 3:1; Afil. 1:10) Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni. (1 Yoh. 5:14) Kusunga nthawi ndi njira imodzi imene imasonyeza kuti timatsatira malamulo awiri akuluakulu, omwe ndi kukonda Mulungu komanso kukonda anzathu.—Mat. 22:37-39.