Sonyezani Kuyamikira Nyumba ya Mulungu
1 M’nthaŵi za Baibulo, Yehova analamulira anthu ake kusonkhana pamodzi nthaŵi zonse panyumba yake. (Lev. 23:2) Misonkhano imeneyi inawathandiza kusunga maganizo awo pa mawu a Mulungu, inawapatsa nthaŵi ya kusinkhasinkha, kuyanjana, ndi kukambitsirana za Chilamulo cha Yehova. Maganizo awo anadzazidwa ndi malingaliro a Mulungu, zimene zinawabweretsera madalitso auzimu ochuluka. Zimenezi zinalidi nthaŵi zachisangalalo. Makonzedwewo anachirikiza umodzi ndi kulambira koyera. Misonkhano m’nyumba ya Mulungu lerolinonso ili yofunika mofananamo.
2 Kodi Tingasonyeze Motani Kuti Timayamikira Misonkhano? Mipingo ina imachitira lipoti ziŵerengero zotsika kwambiri za ofika pamisonkhano, makamaka pa Sukulu Yautumiki Wateokrase, Msonkhano Wautumiki ndi Phunziro Labuku Lampingo. Nthaŵi zina mkhalidwe wa munthu ungamlepheretse kufika pamsonkhano. Koma kodi mwalola mavuto aang’ono kulepheretsa kufika kwanu pamisonkhano mokhazikika? Ena angasankhe kukhala kunyumba ngati amva mutu pang’ono kapena ngati amva kutopa pambuyo pa tsiku lotangwanitsa. Ena akakamizika kucheza ndi achibale osakhulupirira odzacheza. Ena aphonya misonkhano ngakhale kaamba ka kufuna kupenyerera programu imene amakonda pa TV kapena maseŵera ena. Mlingo wa kuyamikira wosonyezedwa m’mikhalidwe imeneyi mwachionekere umapereŵera pa umene unasonyezedwa ndi ana a Kora wakuti: “Moyo wanga ulakalaka, inde ukomokanso ndi kufuna mabwalo a Yehova.”—Sal. 84:2.
3 Ngakhale kuti pali chakudya chauzimu cha mwana alirenji chogaŵiridwa pamisonkhano, ena opezekapo ali ndi vuto la kusatchera khutu. Iwo angayambe kulingalira zinthu zina, kuganizira za nkhaŵa za tsikulo, kapena ngakhale kuwodzera. Ambiri apeza kuti kumalemba nsonga zachidule kumawathandiza kukhala ogalamuka ndi kusumika maganizo pa zimene zikunenedwa. Kulemba zinthu kumakhomerezanso chidziŵitso m’maganizo. Ndiponso, kukonzekera pasadakhale kumathandiza kupindula mokwanira. Ngati tikonzekera bwino, tidzakhala okhoza “kupereka chisamaliro choposa cha nthaŵi zonse.”—Aheb. 2:1, NW.
4 Ana limodzinso ndi achikulire afunikira kumvetsetsa malangizo operekedwa pamisonkhano. Zimene ana amaphunzira zidzakhala zochepa kwambiri ngati makolo awapatsa zoseŵeretsa kapena mabuku ojambulamo zithunzithunzi kuti akhale otangwanidwa ndi kanthu kena kapena kuti akhale chete. Kumakhala kusoŵeka kwa chilango choyenera ngati ana amaloledwa kuseŵera, kulankhula, kulira, kapena kuchita zinthu zina zimene zimasokoneza awo okhala pafupi. Kutuluka kaŵirikaŵiri kupita kuchimbudzi kapena kukamwa madzi mkati mwa misonkhano kumachepa pamene mwana adziŵa kuti mmodzi wa makolo ake adzapita naye.
5 Kufika Panthaŵi Yake Kuli Kofunika: Nthaŵi zina, mikhalidwe yosapeŵeka ingatiletse kufika pamisonkhano panthaŵi yake, koma chizoloŵezi cha kufika pamisonkhano pambuyo pa nyimbo yoyamba ndi pemphero chimasonyeza kusalemekeza chifuno chopatulika cha misonkhano ndi kusasamala za thayo lathu la kupeŵa kusokoneza ena. Kumbukirani kuti kuimba ndi kupemphera pamodzi ndi abale athu pamisonkhano ya mpingo kuli mbali ya kulambira kwathu. Kuchedwa kwachizoloŵezi kumachititsidwa ndi kupanda dongosolo kapena kulephera kulinganiza zinthu pasadakhale. Kufika panthaŵi yake kumasonyeza kuti timalemekeza ndi kuyamikira misonkhano yathu.
6 Pamene tsiku likhala likuyandikirabe, kufunika kwa kusonkhana pamodzi kumakhalanso kukukulirapo. (Aheb. 10:24, 25) Tiyeni tisonyeze chiyamikiro chathu mwa kufika pamisonkhano mokhazikika, kukonzekera pasadakhale, kufika panthaŵi yake, kutchera khutu, ndiyeno kugwiritsira ntchito zimene timaphunzira.