Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/94 tsamba 2
  • Misonkhano Yautumiki ya December

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Misonkhano Yautumiki ya December
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira December 5
  • Mlungu Woyambira December 12
  • Mlungu Woyambira December 19
  • Mlungu Woyambira December 26
Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
km 12/94 tsamba 2

Misonkhano Yautumiki ya December

Mlungu Woyambira December 5

Nyimbo Na. 68

Mph. 12: Zilengezo za pamalopo ndi Zilengezo zoyenera zotengedwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Tchulani nkhani imodzi kapena ziŵiri zokopa maganizo zimene zingasonyezedwe pogaŵira magazini atsopano. Wofalitsa wokhoza bwino achitire chitsanzo ulaliki, akumagwiritsira ntchito imodzi ya nkhanizo.

Mph. 15: “Chitsanzo Chimene Tiyenera Kulondola Mosamalitsa.” Mafunso ndi mayankho.

Mph. 18: “Itanirani Ena Kudzatsatira Munthu Wamkulu Koposa.” Kambitsiranani ndi omvetsera. Konzani zitsanzo ziŵiri zachidule. Gogomezerani kufunika kwa kusunga cholembapo cha kunyumba ndi nyumba cholondola; fotokozani mwachidule zimene ziyenera kulembedwapo.

Nyimbo Na. 153 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira December 12

Nyimbo Na. 86

Mph. 13: Zilengezo za pamalopo ndi Mbiri Yateokrase. Lipoti la maakaunti, kuphatikizapo ziyamikiro za chopereka chilichonse. Perekani malingaliro a mmene tingayankhire moni wa paholide yakudziko.—Onani Utumiki Wathu Waufumu, December, 1990, tsamba 4.

Mph. 14: “Samalirani Chiphunzitso Chanu Nthaŵi Zonse.” Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira sukulu. Longosolani malangizo a mu “Ndandanda ya Sukulu Yautumiki Wateokratiki ya 1995,” mukumatchula zikumbutso zofunikira zilizonse makamaka ku mpingo.

Mph. 18: “Sonyezani Kuyamikira Nyumba ya Mulungu.” Mafunso ndi mayankho. Perekani ndemanga zowonjezera ponena za kufunika kwa kufika panthaŵi yake pamisonkhano.—Onani Nsanja ya Olonda ya June 15, 1990, masamba 26-9.

Nyimbo Na. 99 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira December 19

Nyimbo Na. 78

Mph. 10: Zilengezo za pamalopo. Longosolani makonzedwe a pamalopo a utumiki wakumunda mkati mwa nyengo ya holide ilinkudza. Sonyezani njira zogaŵira magazini atsopano m’gawo la kumaloko.

Mph. 20: “Kuphunzira Buku la Moyo Wanu wa Banja pa Phunziro Labuku Lampingo.” Mphatika. Mafunso ndi mayankho pa ndime 1-8, iperekedwe ndi mkulu. Kambitsiranani tanthauzo la malemba osonyezedwa.

Mph. 15: “Asonkhezereni Kukhala Otsatira Ake.” Kambitsiranani ndi omvetsera. Khalani ndi zitsanzo zachidule ziŵiri. Limbikitsani onse kugwiritsira ntchito ina ya nthaŵi ya utumiki wakumunda pa kupanga maulendo obwereza.

Nyimbo Na. 22 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira December 26

Nyimbo Na. 74

Mph. 5: Zilengezo za pamalopo. Kambitsiranani nkhani yakuti “Kodi Nthaŵi Yanu ya Kusonkhana Idzasintha?” ngati imakhudza mpingo wanu.

Mph. 20: “Kuphunzira Buku la Moyo Wanu wa Banja pa Phunziro Labuku Lampingo.” Mphatika. Mafunso ndi mayankho pa ndime 9-18, iperekedwe ndi mkulu. Gogomezerani kufunika kwa kukonzekera, kupezekapo mokhazikika, ndi kuyankhapo pa Phunziro Labuku Lampingo. Sonyezani kuyamikira malangizo auzimu, ofunika kwenikweni kutitsogolera m’masiku ano amapeto.

Mph. 10: Zosoŵa za pamalopo. Kapena perekani nkhani yakuti “Kodi Mukuthandiza Mwana Wanu Kusankha Yehova?” mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 1994, masamba 26-30.

Mph. 10: Konzekerani Chogaŵira cha mu January. Mungagwiritsire ntchito mabuku alionse a masamba 192 omwe mpingo ungakhale nawo m’sitoko pa 40t monga momwe kwasonyezedwera pa zilengezo. Ngati mpingo ulibe alionse m’sitoko, buku la Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani? lingagaŵiridwe. Ngati bukuli lidzagwiritsiridwa ntchito kwanuko, konzani chitsanzo chimodzi chimene chingagwiritsiridwe ntchito pogaŵira bukulo pakhomo. Ngati buku lina nlimene lidzagaŵiridwa, konzani ulaliki umodzi kapena aŵiri oyenerera a kuligaŵira. Malingaliro operekera ulaliki angapezedwe m’buku la Kukambitsirana, masamba 9-15. Wofalitsa wokhoza bwino achitire chitsanzo ulaliki.

Nyimbo Na. 94 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena