Nyimbo 94
Mfumu Yosatha, Yeretsani Dzina Lanu!
1. Ya ndinu Mulungu yekha,
Kunthaŵi yosadziŵika.
Mwasonyeza chipiliro,
Mpaka mutadziyeretsa.
Chifuno chanu nchosatha;
Ntchitozo zisonya nzeru;
Ufumu wanu wafika,
Kuipa konse kupita.
2. Mlengi waponseponsedi,
Ndinu wakale kaledi!
Mwawona kuipa konse,
Pansi pa mapazi anu.
Mwatipatsa Mwana wanu;
Adzalamula kosatha.
Adzachotsatu adani;
Izi tizipempherera.
3. Aneneri ananena
Za kupulumutsidwatu.
Zikukwaniritsidwadi,
Tikuchitira umboni.
Dziko lathu silidzatha,
Silidzasinthika konse.
Wonetsani ukuluwo,
Dzetsani ulamuliro.