Nyimbo 68
Chifundo Chaumulungu
1. Tikakhaladi Akristu,
Tisonyeze chifundo
Kwa mabwenzi ndi alendo,
Ndi kwa osawadziŵa.
Yesu Mphunzitsiyo
Anamveketsa izi
Mwafanizo lake.
Odala akumvawo.
2. ‘Msamariya winawake
Anamka ku Yeriko.
M’njira anapeza Myuda;
Wofwambidwa panjira.’
Kuti amthandize,
Anachotsa kunyada.
Mwachikondi chake.
Anachita lamulo.
3. Izi zisonyeza mnansi.
Wofuna chithandizo.
Ya ndi wabwino kwa onse,
Apatsa mvula dzuŵa.
Chikondi chakecho!
Ndithudi bwenzi lathu.
Kukoma mtimako.
Pa izi tidalira.
4. Nthaŵi zina tipereka
Chakudya kwa mnansidi.
Kulidi kofulumira,
Kuti apeze moyo.
Kudziŵa Ufumu,
Cho’nadi cha Mulungu
Tipatsa anansi
Kuti atamande Ya.