Nyimbo 78
Kulankhula “Chinenero Choyera”
1. Anthu a Ya ali ndi chinenero,
Choyera ndi cha umodzi.
Mawu ake ngokondweretsa mtima.
Asonkheza chikondano.
2. Yehova apatsa chinenerochi
Kwa awo odzichepetsa.
Poti afunitsitsa kuphunzitsa
Ena chilankhulidwecho.
3. Mikhalidwe yoipa ichotsedwa
Ndi odziŵa chinenero.
Amamatira kunjira za M’lungu.
Nakana njira zadziko.
4. Mogwirizana titumikire Ya.
Atsogoza anthu ake.
Ndi chinenero tilalika mbiri;
Tilankhula uthengawo.