Kodi Nthaŵi Yanu ya Kusonkhana Idzasintha?
Ngati mipingo ingapo imene imagwiritsira ntchito Nyumba Yaufumu imodzi yamvana kumasinthana kapena kusintha nthaŵi ya kusonkhana, chimenechi chiyenera kuchitidwa pa 1 January. Kukhala ofunitsitsa kugwirizana ndi makonzedwe amene akhazikitsidwa kumasonyeza kukondana ndi kulingalirana. Kaŵirikaŵiri kusintha kwa nthaŵi ya kusonkhana kudzakhala bwino kumbali yanu, kukumachititsa kupezeka pamisonkhano kukhala kosavuta.
Komano, mwinamwake kusintha kumene kukuchitika chaka chino sikungayenerane bwino ndi programu ya zochita zanu. Mungafunikire kupanga masinthidwe pa zochita zanu amene mwina sangakukhalireni bwino kwenikweni. Kufunitsitsa kwa aliyense kugwirizana kumasonyeza kuyamikira makonzedwe onse, kumene kumapindulitsa aliyense woloŵetsedwamo.
Indedi, kusinthana nthaŵi ya kusonkhana kotsatira kungadzakuyendereni bwino. Pakali pano, mukulimbikitsidwa kupanga masinthidwe aumwini ofunika kotero kuti mukhale wokhoza kumapezeka pamisonkhano yonse ya mlungu ndi mlungu malinga ndi ndandanda imene yasankhidwa ndi mpingo. Yesayesani kukhala ndi kaonedwe ka wamasalmo Davide, yemwe analengeza kuti: “Ndinakondwera mmene ananena nane, Tiyeni ku nyumba ya Yehova.”—Sal. 122:1.