Mbiri Yateokrase
Albania: Chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa 353 chinafikiridwa mu July, limodzinso ndi chiŵerengero chapamwamba cha magazini ogaŵiridwa. Ofalitsa a mpingo anachita avareji ya maola 22.4 mu utumiki ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo apanyumba 1,073.
Cameroon: Ofesi yanthambi yatsopano inakhazikitsidwa mu July, ikumapezana ndi chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa 21,323.
Greenland: Ofalitsa opereka lipoti la utumiki wakumunda anafika pa 134 mu July. Ichi chinali chiŵerengero chapamwamba chatsopano.
Zaire: Ngakhale kuti anali ndi mkhalidwe watsoka wa othaŵa kwawo zikwi mazana ambiri akumaloŵa mu Zaire, chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa 83,442 chinafikiridwa mu July. Abalewo achita kuyesayesa kwamphamvu pakuthandizana, ndipo akunena kuti akuyamikira kwambiri chithandizo chochokera kunja.