Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/95 tsamba 6
  • Lingalirani za Ena—mbali 1

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Lingalirani za Ena—mbali 1
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Nyumba ya Ufumu Yanu Mumaiona Bwanji?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Malo Olambirira Yehova
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Tiyeni Tizikonza Malo Athu Olambirirapo
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Tizilemekeza Malo Athu Olambirira Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
km 1/95 tsamba 6

Lingalirani za Ena—mbali 1

1 Tikukondwa kuona chipambano cha anthu a Yehova, chimene chachititsa mipingo kuwonjezereka. M’madera ena, makamaka m’mizinda yaikulu, Nyumba Zaufumu zikugwiritsiridwa ntchito mopanikiza, nthaŵi zina mipingo yochulukirapo ikumagwiritsira ntchito Nyumba Yaufumu imodzi. Mkhalidwe umenewu umafuna kuti onse oloŵetsedwamo azilingalirana kwambiri.

2 Mpingo uliwonse umene ukugwiritsira ntchito Nyumba Yaufumu uyenera kuisiya ili yaudongo ndi yokonzedwa bwino kaamba ka abale otsatirapo. Mipando iyenera kuikidwa mwadongosolo, mabuku alionse pa kauntala ayenera kuchotsedwapo, ndipo zinthu zilizonse zaumwini zosiyidwa apa ndi apa m’Nyumba Yaufumu ziyenera kutengedwa. Zimbudzi ziyenera kusiyidwa zili zaudongo, mukumatsimikizira kuti sopo, mataulo, ndi mapepala a m’chimbudzi zaikidwamo ndi kuti zinyalala m’zitini zake zatayidwa.

3 Ngati mpingo wina ukuyamba msonkhano wawo posapita nthaŵi, awo otsalira pambuyo pa msonkhano woyamba sayenera mosafunikira kuzengereza kuchoka, akumadodometsa awo amene akukonzekera msonkhano wotsatira. Makambitsirano akucheza otalikirapo angachititse anthu kudzaza pabalanda ndi kuchedwetsa abale amene akukonzekera kuyamba msonkhano wotsatira. Malo oimikapo galimoto pa Nyumba Yaufumu angakhale aang’ono, ndipo kungakhale kukoma mtima kuchoka msanga kuti amene akufika apeze malo oimikapo galimoto. Komanso, amene akuloŵa msonkhano wotsatira sayenera kufika mwamsanga kwambiri, akumachititsa anthu kudzaza mosafunikira m’balanda ndi galimoto kudzaza pamalo awo.

4 Kumene kuli mipingo yochulukirapo, pali kufunikira kwapadera kwa kugwirizana kwambiri popanga makonzedwe a mlungu ndi mlungu a kuyeretsa Nyumba Yaufumu. Kaŵirikaŵiri, mipingo imasinthana kwa nyengo yoikika. Pamene mpingo wanu uli ndi thayo limenelo, tsimikizirani kuti kuyeretsako kuchitidwa bwino lomwe ndipo mwamsanga kuti mipingo ina yogwiritsira ntchito holoyo isakhale ndi chifukwa chodandaulira.

5 Nthaŵi zina mpingo uliwonse umafunikira kusintha nthaŵi yawo ya msonkhano, monga ngati pamaulendo a woyang’anira dera. Ngati mpingo wina ukukhudzidwa, akulu ayenera kudziŵitsa akulu a mpingo winawo pasadakhale kuti iwo adziŵitse ofalitsa awo mwamsanga ndithu. Ndiponso, ngati chochitika china chovomerezedwa, monga ngati Sukulu ya Utumiki Waupainiya, kukumana kwa akulu a m’deralo, kapena ukwati, chalinganizidwa, mipingo ina ndi oyang’anira madera okhudzidwa ayenera kudziŵitsidwa pasadakhale; chotero sadzalinganiza kugwiritsira ntchito Nyumba Yaufumu panthaŵi imodzimodziyo.

6 Pali maholo ambiri amene amagwiritsiridwa ntchito ndi mipingo ya m’madera osiyana. Nkofunika kuti oyang’anira oyendayenda ochezera mipingo imeneyi azidziŵitsana za kucheza kotsatira kumene akukulinganiza. Masinthidwe anthaŵi itatha kale kapena zovuta zina zingabuke pamene oyang’anira oyendayenda aŵiri alinganiza maulendo awo mu mlungu umodzimodziwo.

7 Kulingalira ena mwachikondi, limodzi ndi kulankhulana kwabwino, kukonzekera kwapasadakhale ndi kugwirizanika kudzathandiza kusunga unansi wabwino pakati pa mipingo ndipo kudzatsimikiziritsa kuti “zonse zichitike koyenera ndi kolongosoka.”—1 Akor. 14:40.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena