Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/94 tsamba 1
  • Chitsanzo Chimene Tiyenera Kulondola Mosamalitsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chitsanzo Chimene Tiyenera Kulondola Mosamalitsa
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
  • Nkhani Yofanana
  • Kulitsani Luso la Kuphunzitsa
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • ‘Tsatirani Mapazi Ake Mosamalitsa’
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • “Ndakupatsani Inu Chitsanzo”
    Nsanja ya Olonda—2002
  • “Nthawi Zonse Iye Ankalankhula Nawo Pogwiritsa Ntchito Mafanizo”
    ‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
km 12/94 tsamba 1

Chitsanzo Chimene Tiyenera Kulondola Mosamalitsa

1 Mosakayika konse, Yesu anali munthu wamkulu koposa onse amene anakhalako. Iye anapereka chitsanzo changwiro kwa ophunzira ake. Ngakhale kuti sititha kufika pamuyezo wa ungwiro wake, tikulimbikitsidwa ‘kulondola mapazi ake.’ (1 Pet. 2:21) Tiyenera kukhala ndi chikhumbo cha kufanana kwambiri ndi Yesu, tikumagaŵira choonadi kwa ena mwachangu.

2 Yesu sanali mlaliki chabe; analinso mphunzitsi wopambana. “Makamu a anthu anazizwa ndi chiphunzitso chake.” (Mat. 7:28) Kodi nchifukwa ninji iye anali wogwira mtima kwambiri? Tiyeni tipende mosamalitsa ‘kaphunzitsidwe kake.’

3 Mmene Tingalondolere Yesu: Yesu anaphunzitsidwa ndi Atate wake. (Yoh. 8:28) Cholinga chake chinali kulemekeza Yehova ndi kukweza dzina Lake. (Yoh. 17:4, 26) Pamene tikuphunzitsa ndi kulalikira, cholinga chathu chiyenera kukhalanso kulemekeza Yehova ndipo osati kukopera maganizo a anthu kwa ife eni.

4 Chilichonse chimene Yesu anaphunzitsa chinali chozikidwa pa Mawu a Mulungu. Iye nthaŵi zonse anatchula zolembedwa m’Malemba. (Mat. 4:4, 7; 19:4; 22:31) Tikufuna kupereka maganizo a omvetsera athu ku Baibulo; motero tikumawalola kuona kuti zimene tikulalikira nzozikidwa pa ulamuliro wopambana koposa.

5 Yesu anagwiritsira ntchito mawu achidule, ogwira ntchito, ndi osavuta. Mwachitsanzo, pofotokoza mmene tingapezere chikhululukiro cha Mulungu, anatilimbikitsa kuti ifenso tikhale okhululukira ena. (Mat. 6:14, 15) Tiyenera kuyesa kufotokoza uthenga wa Ufumu m’mawu osavuta ndi ozoloŵereka.

6 Yesu anagwiritsira ntchito mwaluso mafanizo ndi mafunso kuti asonkhezere ena kulingalira. (Mat. 13:34, 35; 22:20-22) Mafanizo onena za zinthu zozoloŵereka ndi za nthaŵi zonse angathandize anthu kumvetsetsa ziphunzitso zovuta za Baibulo. Tiyenera kufunsa mafunso amene amalimbikitsa omvetsera athu kulingalira ponena za zimene amamva. Mafunso otsogolera angawathandize kufika pazigamulo zoyenera.

7 Yesu anatenga nthaŵi akulongosola zinthu zovuta kwa amene anafunsira kudziŵa zowonjezereka. Amene anali ofunitsitsa, monga ophunzira ake, anali okhoza kupeza lingaliro la zimene Yesu anaphunzitsa. (Mat. 13:36) Nafenso tiyenera kukhala othandiza pamene mafunso afunsidwa moona mtima. Ngati sitidziŵa mayankho ake, tikhoza kufufuza nkhaniyo ndi kudzabwererako ndi mayankho panthaŵi ina.

8 Yesu anagwiritsira ntchito maphunziro a kuchita zinthu pophunzitsa. Chitsanzo cha zimenezi chinali kusambitsa kwake mapazi a ophunzira ake, ngakhale kuti iye anali Mbuye wawo. (Yoh. 13:2-16) Ngati tisonyeza mzimu wodzichepetsa, amene akuphunzitsidwa adzasonkhezereka kugwiritsira ntchito zimene amaphunzira.

9 Yesu anakopa mitima ya anthu ndi chikondi chawo cha chilungamo. Nafenso tikufuna kufikira mitima. Timayesa kukopa chikhumbo cha chibadwa cha anthu onse cha kulambira Mulungu ndi kukhala pamodzi ndi ena mwamtendere ndi chimwemwe.

10 M’December, tikhoza kuuzako ena zinthu zimene taphunzira ponena za Yesu mwa kugaŵira buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Kutsanzira kwathu njira za kaphunzitsidwe ka Yesu kungasonkhezere oona mtima kutchera khutu pamene tikufotokoza zimene iye anaphunzitsa.—Mat. 10:40.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena