Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/95 tsamba 2
  • Mayendedwe Anu Ayenere uthenga Wabwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mayendedwe Anu Ayenere uthenga Wabwino
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Sonyezani Kuyamikira Nyumba ya Mulungu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
  • Khalidwe Labwino Lili Chizindikiro Chapadera cha Anthu a Mulungu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Khalani Aulemu Pamalo Olambirira Yehova
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Yesetsani Kuti Muzisunga Nthawi
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
km 11/95 tsamba 2

Mayendedwe Anu Ayenere uthenga Wabwino

1 Monga Mboni za Yehova, timafuna kupereka ulemu ku dzina la Yehova. Timadziŵa kuti khalidwe lathu, kalankhulidwe, kapesedwe, ndi kavalidwe zingasonkhezere mmene ena amaonera kulambira koona. Makamaka zimenezi zili choncho pamene tili pamisonkhano yathu. Tikufuna kuonetsetsa kuti zonse zimene zikunenedwa ndi kuchitidwa pamisonkhano nzoyenerera uthenga wabwino ndipo zimapereka ulemu kwa Yehova.—Afil. 2:4.

2 Miyezo yambiri ya dziko ya kavalidwe ndi kapesedwe njosavomerezedwa ndi Akristu. Imeneyi ndi nkhani imene iyenera chisamaliro cha atumiki a uthenga wabwino. Nsanja ya Olonda ya June 1, 1989, tsamba 20, inati: “Zovala zathu sizifunikira kukhala za mtengo, koma ziyenera kukhala zaudongo, zabwino, ndi zachikatikati. Nsapato zathu ziyeneranso kukhala mumkhalidwe wabwino ndi zowoneka bwino. Mofananamo, pamisonkhano yonse, kuphatikizapo pa Phunziro Labukhu la Mpingo, matupi athu ayenera kukhala audongo, ndipo tifunikira kuvala mwaukhondo ndi moyenera.”

3 Kusunga nthaŵi kuli chizindikiro cha kulingalira ena kwachikondi. Nthaŵi zina, mikhalidwe yosapeŵeka ingatiletse kufika pamisonkhano panthaŵi yake. Koma chizoloŵezi cha kufika mochedwa chingasonyeze kuti sitilemekeza chifuno chopatulika cha misonkhano ndi kulephera kwathu kuzindikira thayo lathu la kupeŵa kucheukitsa ena. Kaŵirikaŵiri ofika mochedwa amacheukitsa ena ndi kuwadodometsa kupindula mokwanira m’programu. Kusunga nthaŵi kumasonyeza ulemu pa malingaliro ndi zokonda za omvetsera onse.

4 Kukonda anansi athu kuyenera kutichititsa kupeŵa mosamala kucheukitsa ena mkati mwa misonkhano. Kunong’ona, kudya, kutafuna chingamu, kuliza mapepala, ndi kupitapita kuchimbudzi kosafunikira kungadodometse kuchita tcheru kwa ena ndi kuwacheukitsa pa ulemu wofunikira kuperekedwa pamalo olambirira Yehova. Kuli kosayenera kwa aliyense kuchita zinthu zina za mpingo kapena kukambitsirana ndi ena kusiyapo ngati pali chinthu china chamwadzidzidzi chimene chikufuna kuti abale achoke pamalo awo. Komabe, onse ayenera kukhala pansi ndi kumamvetsera programu kuti iwo eni ndi mabanja awo apindule. Makhalidwe oipa safunika m’Nyumba Yaufumu chifukwa chakuti “chikondi . . . sichichita zosayenera.”—1 Akor. 13:4, 5; Agal. 6:10.

5 Khalidwe labwino la ana athu pamisonkhano limaperekanso chitamando ndi ulemu pa dzina la Yehova. Uyang’aniro wamphamvu wa makolo ngwofunika. Ana ayenera kulimbikitsidwa kumvetsera ndi kutengamo mbali. Makolo ambiri okhala ndi ana aang’ono amasankha kukhala pamalo pamene angathe kuchokapo mosavuta ndi kukasamalira zimene ana awo akufunikira popanda kucheukitsa ena kwakukulu.

6 Paulo analangiza kuti: “Mayendedwe anu ayenere uthenga wabwino.” (Afil. 1:27) Pamenepo, tiyenitu tiyeseyese kukhala amayendedwe abwino ndi olingalira ena pamene tifika pamisonkhano. Kugwirizanika kochitidwa ndi onse kudzasonyezadi kuti padzakhala ‘kulimbikitsana . . . kochitidwa ndi aliyense mwa chikhulupiriro cha mnzake.’—Aroma 1:12, NW.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena