Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/15 tsamba 7
  • Zinthu Zomwe Timagwiritsa Ntchito Pophunzitsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zinthu Zomwe Timagwiritsa Ntchito Pophunzitsa
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Nkhani Yofanana
  • Tiziphunzitsa Mfundo za Choonadi
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • Tizigwiritsa Ntchito Mwaluso Zinthu Zomwe Timagwiritsa Ntchito Pophunzitsa
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • Muzigwiritsa Ntchito Zinthu Zofufuzira
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Muzigwira Ntchito Yanu Mwaluso
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
km 7/15 tsamba 7

Zinthu Zomwe Timagwiritsa Ntchito Pophunzitsa

1. Kodi Akhristufe tikufanana bwanji ndi amisiri?

1 Mmisiri amakhala ndi zipangizo zosiyanasiyana zomwe amagwiritsa ntchito. Zina mwa zipangizozi sazigwiritsa ntchito kawirikawiri poyerekezera ndi zina. Amisiri odziwa bwino ntchito yawo amaonetsetsa kuti nthawi zonse ali ndi zipangizo zomwe amagwiritsa ntchito kawirikawiri, choncho amazizolowera ndipo amazigwiritsa ntchito mwaluso kwambiri. Baibulo limatilimbikitsa Akhristufe kuti tizidzipereka pa utumiki wathu. Limatilimbikitsanso kuti tikhale “wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi.” (2 Tim. 2:15) Ndiye kodi chipangizo chofunika kwambiri chomwe timagwiritsa ntchito ndi chiti? Ndi Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu. Timagwiritsa ntchito Baibulo ‘pophunzitsa anthu kuti akhale ophunzira’ a Yesu. (Mat. 28:19, 20) Choncho tiyenera kuyesetsa kuti tikhale aluso ‘pophunzitsa ndi kufotokoza bwino mawu a choonadi.’ Koma tilinso ndi zinthu zina zomwe tonsefe tiyenera kuphunzira kuzigwiritsa ntchito mwaluso pophunzitsa anthu choonadi.—Miy. 22:29.

2. Tchulani zinthu zimene timagwiritsa ntchito kwambiri pophunzira ndi anthu.

2 Zinthu Zina Zomwe Timagwiritsa Ntchito Pophunzitsa: Kuwonjezera pa Baibulo, kodi ndi zinthu zina ziti zomwe timagwiritsa ntchito? Buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? ndi lomwe timaligwiritsa ntchito kwambiri pophunzitsa anthu mfundo za m’Baibulo. Tikamaliza kuphunzira bukuli ndi munthu, tiyenera kuyamba kuphunzira naye buku lakuti, Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’? Cholinga ndi kum’phunzitsa kuti azitsatira mfundo za m’Baibulo pa moyo wake. Koma kuti zonsezi zitheke, tiyenera kuphunzira kugwiritsa ntchito mwaluso mabukuwa. Tilinso ndi timabuku tina tomwe tiyenera kutigwiritsa ntchito kawirikawiri. Mwachitsanzo kabuku kakuti, Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu kamatithandiza kwambiri poyambitsa maphunziro. Ngati m’gawo lathu muli anthu amene amavutika kuwerenga kapena omwe amalankhula chinenero choti tilibe mabuku ambiri a chinenerocho, tingathe kugwiritsa ntchito kabuku kakuti, Mverani Mulungu kapena Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha. Kabuku komwe timagwiritsa ntchito kwambiri pothandiza anthu omwe timaphunzira nawo Baibulo kuti adziwe bwino gulu la Mulungu ndi kakuti, Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano? Palinso mavidiyo omwe tingagwiritse ntchito kuthandiza anthu kuti akhale ophunzira a Yesu, ndipo tiyenera kuyesetsa kuti tiziwagwiritsa ntchito mwaluso. Ena mwa mavidiyowa ndi monga yakuti, Kodi Mulungu Ali ndi Dzina?, Kodi pa Nyumba ya Ufumu Pamachitika Zotani? ndi yakuti, N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo?

3. Kodi nkhani zomwe zidzatuluke mu Utumiki wa Ufumu wa kutsogoloku zidzatithandiza bwanji?

3 Mu Utumiki wa Ufumu wa kutsogoloku, muzidzakhala nkhani zomwe zidzatithandize kudziwa mmene tingagwiritsire ntchito mwaluso zinthu zomwe timazigwiritsa ntchito kwambiri pophunzitsa. Tikamayesetsa kugwiritsa ntchito zinthu zimenezi mwaluso, ndiye kuti tikutsatira malangizo akuti: “Nthawi zonse uzisamala ndi zimene umachita komanso zimene umaphunzitsa. Pitiriza kuchita zimenezi, chifukwa ukatero udzadzipulumutsa wekha komanso anthu okumvera.”—1 Tim. 4:16.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena