MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Muzigwira Ntchito Yanu Mwaluso”
Kalipentala waluso amadziwa mmene angagwiritsire ntchito zipangizo zake. Mofanana ndi zimenezi, mtumiki wa Yehova amakhala “wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi ndi ntchito imene wagwira” ngati amadziwa kugwiritsira ntchito bwino Zinthu Zophunzitsira. (2 Tim. 2:15) Yankhani mafunso otsatirawa kuti muone ngati mumadziwa kugwiritsa ntchito bwino zinthu zomwe timagwiritsira ntchito pophunzira ndi anthu mu utumiki.
MVERANI MULUNGU KUTI MUDZAPEZE MOYO WOSATHA
Kodi kabukuka tingakagwiritsire ntchito pophunzira ndi anthu ati?—mwb17.03 5 ¶1-2
Kodi tingakagwiritsire ntchito bwanji tikamaphunzira ndi anthu?—km 7/12 3 ¶6
Kuwonjezera pa kabukuka, kodi ndi mabuku enanso ati omwe tiyenera kuphunzira ndi munthu kuti afike pobatizidwa?—km 7/12 3 ¶7
UTHENGA WABWINO WOCHOKERA KWA MULUNGU
Kodi kabukuka ndi kosiyana bwanji ndi zinthu zina zomwe timagwiritsira ntchito pophunzira ndi anthu?—km 3/13 4-5 ¶3-5
N’chiyani chomwe muyenera kuchita mukamagawira kabukuka?—km 9/15 3 ¶1
Kodi mungagwiritsire ntchito bwanji kabukuka mukamaphunzira ndi anthu?—mwb16.01 8
Kodi tingayambe liti kuphunzira buku la Zimene Baibulo Limaphunzitsa?—km 3/13 7 ¶10
ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA
Kodi tingagwiritsire ntchito bwanji mfundo zachidule za m’bukuli komanso mawu akumapeto?—mwb16.11 5 ¶2-3
KODI NDANI AKUCHITA CHIFUNIRO CHA YEHOVA MASIKU ANO?
Kodi tingayambe liti kuphunzira ndi munthu kabuku kameneka?—mwb17.03 8 ¶1
Kodi kabukuka tingakagwiritsire ntchito bwanji?—mwb17.03 8, kabokosi