-
Ndandanda ya Mlungu wa March 25Utumiki wa Ufumu—2013 | March
-
-
Ndandanda ya Mlungu wa March 25
MLUNGU WOYAMBIRA MARCH 25
Nyimbo Na. 33 and Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 20 ndime 16-20 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Luka 4-6 (Mph. 10)
Na. 1: Luka 4:22-39 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Mitundu ya Anthu Inachokera Kuti?—rs tsa. 234 ndime 2-tsa. 235 ndime 1 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Pali Umboni Wotani Wosonyeza Kuti Yesu Anaukitsidwa?—1 Akor. 15:3-7 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Yambitsani Phunziro la Baibulo Loweruka Loyambirira. Pogwiritsa ntchito chitsanzo cha ulaliki chimene chili patsamba 8, chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungayambitsire phunziro la Baibulo Loweruka loyambirira m’mwezi wa April. Limbikitsani abale ndi alongo onse kuti adzayesetse kuyambitsa nawo maphunziro a Baibulo.
Mph. 25: “Gwiritsani Ntchito Kabuku Kakuti Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu.” Mafunso ndi mayankho. Mukamakambirana ndime 6, chitani zitsanzo ziwiri.
Nyimbo Na. 97 ndi Pemphero
-
-
Gwiritsani Ntchito Kabuku Kakuti Uthenga Wabwino Wochokera kwa MulunguUtumiki wa Ufumu—2013 | March
-
-
3. Kodi kabukuka kakusiyana bwanji ndi mabuku ena?
3 Kodi Kalembedwa Bwanji? Mabuku athu ambiri alembedwa m’njira yoti munthu angawawerenge n’kumvetsa choonadi popanda kuthandizidwa ndi munthu wina. Koma si mmene kalili kabukuka. Kalembedwa kuti munthu aziphunzira mothandizidwa ndi munthu wina. Choncho mukamapereka kabukuka ndi bwino kukambirana ndi munthuyo ndime imodzi kapena ziwiri. Ndime zake ndi zifupizifupi moti mukhoza kukambirana ndi munthu mutangoimirira kapena ali kuntchito. Ngakhale kuti ndi bwino nthawi zambiri kuyamba kuphunzira ndi munthu pa phunziro 1, mutha kuyamba ndi phunziro lililonse.
4. Kodi kabukuka kadzatithandiza bwanji kuphunzitsa kuchokera m’Baibulo?
4 M’mabuku athu ambiri, mayankho a mafunso amakhala m’ndime. Koma m’kabukuka, mayankho amapezeka nthawi zambiri m’Baibulo. Anthu ambiri amafuna kumva zinthu kuchokera m’Baibulo osati m’mabuku athu. Choncho, ndi malemba ochepa kwambiri amene awagwira mawu. Cholinga n’choti tiziwerenga m’Baibulo lenilenilo. Izi zidzathandiza anthu kudziwa kuti akuphunzitsidwa ndi Mulungu.—Yes. 54:13.
5. N’chifukwa chiyani tiyenera kukonzekera bwino phunziro lililonse?
5 Kabukuka sikafotokoza malemba onse. Achita dala zimenezi pofuna kuti wophunzira azifunsa mafunso ndipo wophunzitsayo aziyankha mwaluso. Choncho kukonzekera bwino phunziro lililonse n’kofunika. Koma tiyenera kusamala kuti tisamachulukitse gaga m’diwa pofotokoza zinthu. Pajatu ife timakonda kwambiri kufotokoza Malemba. Koma zingakhale zothandiza kwambiri ngati titapempha wophunzirayo kuti afotokoze maganizo ake pa lembalo. Tizigwiritsa ntchito mafunso mwaluso kuti timuthandize kumvetsa malemba.—Mac. 17:2.
-