Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • rs tsamba 234-tsamba 239
  • Mafuko a Anthu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafuko a Anthu
  • Kukambitsirana za m’Malemba
  • Nkhani Yofanana
  • Pamene Mafuko Onse Adzakhala Pamodzi Pamtendere
    Galamukani!—1993
  • Adamu ndi Hava
    Kukambitsirana za m’Malemba
  • Kodi Mkazi wa Kaini Anali Ndani?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Mdani Wathu Womalizira Adzawonongedwa
    Nsanja ya Olonda—2014
Onani Zambiri
Kukambitsirana za m’Malemba
rs tsamba 234-tsamba 239

Mafuko a Anthu

Tanthauzo: Monga momwe lagwiritsidwira ntchito pano, fuko limatanthauza chigawo cha anthu amene mogwirizana ndi zikhoterero zakuthupi zimene zingakhale zacholoŵa ndi zimene ziri zokwanira kulekanitsa kaguluko kukhala mtundu wa anthu wapawokha. Komabe, kuyenera kudziŵika, kuti chenicheni chakuti mafuko ali okhoza kukwatirana moloŵana ndi kukhoza kubala ana chimasonyeza kuti kwenikweni iwo ali “mtundu” umodzi iwo onse amakhala a banja laumunthu. Chotero mafuko osiyanasiyana ali mbali chabe za kusiyanasiyana konse kothekerako mwa anthu.

Kodi mafuko osiyanasiyana anachokera kuti?

Gen. 5:1, 2; 1:28: “Tsiku lomwe Mulungu analenga munthu anamlenga m’chifanizo cha Mulungu; anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi, nawadalitsa iwo natcha mtundu wawo anthu, tsiku lomwe anawalenga iwo.” “Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.” (Chotero anthu onse ali mbadwa za anthu oyambirira amenewo, Adamu ndi Hava.)

Mac. 17:26, NW: “[Mulungu] anapanga kuchokera mwa munthu mmodzi [Adamu] mtundu uliwonse wa anthu, kuti ukhale ponse pankhope ya dziko lapansi.” (Chotero, mosasamala kanthu za mafuko amene amapanga mtunduwo, iwo onse ali mbadwa za Adamu.)

Gen. 9:18, 19: “Ana aamuna a Nowa amene anatuluka m’chingalaŵa ndiwo Semu, ndi Hamu, ndi Yafeti. . . . Ameneŵa ndiwo ana aamuna atatu a Nowa; ndiwo anafalikira dziko lonse lapansi.” (Mulungu atatha kuwononga dziko losapembedza mwa chigumula cha padziko lonse m’tsiku la Nowa, chiŵerengero chatsopano cha anthu cha dziko lapansi, kuphatikizapo mafuko onse odziŵika lerolino, chinachokera kumbadwa za ana aamuna atatu a Nowa ndi akazi awo.)

Kodi Adamu ndi Hava anali anthu ongoyerekezera (ongopeka)?

Baibulo silimachirikiza lingaliro limeneli, wonani mutu waukulu wakuti “Adamu ndi Hava.”

Kodi Kaini anapeza kuti mkazi wake ngati panali banja limodzi lokha?

Gen. 3:20: “Mwamuna [Adamu] anamutcha dzina la mkazi wake, Hava; chifukwa ndiye amake wa amoyo onse.” (Motero anthu onse anayenera kukhala mbadwa za Adamu ndi Hava.)

Gen. 5:3, 4: “Adamu anakhala ndi moyo zaka zana limodzi kudza makumi atatu, nabala mwana wamwamuna, m’chifanizo chake; namtcha dzina lake Seti. Masiku ake Adamu atabala Seti, anali zaka mazana asanu ndi atatu; ndipo anabala ana aamuna ndi aakazi.” (Mmodzi wa ana aamuna a Adamu anali Kaini, ndipo mmodzi wa ana aakazi a Adamu ayenera kukhala atakhala mkazi wa Kaini. Panthaŵiyo m’mbiri ya anthu pamene anthu anali chikalirebe ndi thanzi labwino lakuthupi ndi nyonga, monga momwe kukusonyezedwera ndi kutalika kwa zaka za moyo wawo, kuthekera kwa kupitirizira zirema zathupi chifukwa cha kukwatirana ndi mbale wapafupi sikunali kwakululu. Komabe, pambuyo pa zaka 2 500 za mbiri ya anthu, pamene mkhalidwe wakuthupi wa anthu unali utaipa kwambiri, Yehova anapereka malamulo kwa Israyeli oletsa ukwati wapachibale.)

Gen. 4:16, 17, NW: “Kaini anachoka pamaso pa Yehova, nakhala m’dziko Lothaŵirako (kapena Nodi) chakummaŵa kwa Edene. Pambuyo pake Kaini anagona ndi mkazi wake [“anadziŵa mkazi wake,” ndiko kuti, mwaubwenzi, KJ, RS; “anagona ndi mkazi wake,” NE] ndipo anatenga pakati nabala Enoki.” (Wonani kuti Kaini sanakumane ndi mkazi wake kwa nthaŵi yoyamba m’dziko limene anathaŵira, monga ngati kuti anachokera kubanja lina. Mmalo mwake, kunali kumeneko kumene anagona naye nabala mwana wa mwamuna.)

Kodi nchiyani chimene chiri magwero a kusiyana kwa mikhalidwe yamafuko?

“Anthu onse okhala ndi moyo lerolino ngamtundu umodzi Homo sapiens, ndipo achokera ku magazi ofanana. . . . Kusiyana m’kaumbidwe pakati pa anthu kumachititsidwa ndi mpangidwe wacholoŵa ndi chiyambukiro cha mkhalidwe wa malo okhala pamajini. M’zochitika zambiri, kusiyana kumeneko kwachititsidwa ndi kugwira ntchito mogwirizana kwa zinthu ziŵiri zimenezi. . . . Kaŵirikaŵiri kusiyana pakati pa anthu a fuko lofanana kapena mkati mwa anthu kuli kokulirapo kwambiri kuposa avereji ya kusiyana pakati pa mafuko kapena anthu.”—Gulu lamitundu yonse la asayansi losonkhanitsidwa ndi UNESCO, logwidwa mawu mu Statement on Race (New York, 1972, kope lachitatu), Ashley Montagu, pp. 149, 150.

“Fuko ndilo kokha chimodzi cha zochititsa zamajini zosiyanasiyana m’chimene fuko la anthu linagaŵanikiramo mkati ndi motsatizana ndi kufalikira kwawo koyambirira m’zigawo zosiyanasiyana zokhala kwawo. Fuko limodzi latuluka kuchokera m’lirilonse la zigawo zazikulu zisanu za dziko lapansi. . . . Ndithudi munthu anasintha mogwirizana ndi majini mkati mwa nyengo imeneyi ya m’mbiri ndipo tingathe kupima ndi kupenda zotulukapo za mafuko akale mogwirizana ndi malo a dziko. Monga momwe tikayembekezerera, kusinthako kukuwonekera kukhala kogwirizanitsidwa ndi mlingo wa kulekanitsidwa. . . . Pamene kusinthika kwa mafuko kunachitika m’zigawozo, ndi kugwirizanitsidwa kwa anthu zikwi mazana ambiri m’kusiyana kwawo kwa majini kopitirizidwa padziko lonse lapansi, kusiyana kwa mawonekedwe amajini kumene timawona tsopano kunayambika. . . . Vuto limene tayang’anizana nalo nlakuti kagulu kalikonse ka anthu kamawonekera kukhala kosiyana kunja chikhalirechobe pansi pa kusiyana kumeneko pali kufanana kwakukulu.” (Heredity and Human Life, New York, 1963, H. L. Carson, pp. 151, 154, 162, 163) (Motero, kuchiyambiyambi kwa mbiri ya anthu, pamene kagulu ka anthu kanalekanitsidwa ndi ena ndi kukwatira mkati mwa kaguluko, kugwirizana kotsimikizirika kwapadera kwa ziyambukiro za majini kunakhomerezeka mkati mwawo.)

Kodi Baibulo limaphunzitsa kuti akuda ngotembereredwa?

Lingaliro limenelo lazikidwa pa kusamvetsetsedwa kwa Genesis 9:25, pamene Nowa akugwidwa mawu kukhala akunena kuti: “Wotembereredwa ndi Kanani: adzakhala kwa abale ake kapolo wa akapolo.” Paŵerengeni mosamalitsa; sipamanena kanthu ponena za mawonekedwe a khungu. Themberero linali chifukwa chakuti mwana wamwamuna wa Hamu Kanani mwachiwonekere anali atachita kachitidwe kochititsa manyazi koyenerera themberero. Koma kodi ndani amene anali mbadwa za Kanani? Osati akuda, koma anthu akhungu loyera okhala chakummaŵa kwa Nyanja Yaikulu. Chifukwa cha zizoloŵezi zawo zoluluzika, mazoma awo auchiŵanda, kulambira mafano, ndi kupereka nsembe ana, iwo anaweruzidwa ndi Mulungu, ndipo Mulungu anapereka dziko limene Akanani anali kukhalamo kwa Israyeli. (Gen. 10:15-19) Si Akanani onse amene anawonengedwa; ena analoŵetsedwa mu ukapolo, mokwaniritsa themberero limeneli.—Yoswa 17:13.

Kodi akuda anachokera kwa mwana uti wa Nowa? “Ana amuna a Kusi [mwana wina wamwamuna wa Hamu]: Seba, ndi Havila, ndi Sabita, ndi Raama, ndi Sabiteka.” (Gen. 10:6, 7) Kaŵirikaŵiri maumboni a malemba a Baibulo apambuyo pake onena za Kusi amayenerera Etiyopia. Seba akugwiritsiridwa ntchito pambuyo pake potchula anthu ena okhala chakummaŵa kwa Afirika ndipo mwachiwonekere kufupi ndi ku Etiyopiya.—Yes. 43:3, mawu amtsinde m’kope la Malifarensi la NW.

Kodi anthu onse ali ana a Mulungu?

Kukhala ana a Mulungu sindiko kanthu kena kamene anthu opanda ungwirofe tiri okayenerera mwa kubadwa. Koma tonsefe tiri mbadwa za Adamu, amene pamene analengedwa ali wangwiro anali “mwana wa Mulungu.”—Luka 3:38.

Mac. 10:34, 35: “Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wokumuopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.”

Yoh. 3:16: “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Kusonyeza chikhulupiriro chowona mwa iye kuli kofunika kuti aliyense wa ife apeze mtundu wa unansi ndi Mulungu umene Adamu anataya. Mwaŵi umenewo ngwotsegukira anthu amafuko onse.)

1 Yoh. 3:10: “Mmenemo amawoneka ana a Mulungu, ndi ana a Mdyerekezi: yense wosachita chilungamo siali wochokera kwa Mulungu; ndi iye wosakonda mbale wake.” (Chotero Mulungu samawona anthu onse kukhala ana ake. M’lingaliro lauzimu, awo amene mwadala amachita zinthu zimene Mulungu amatsutsa atate wawo ndiye Mdyerekezi. Wonani Yohane 8:44. Komabe, Akristu owona amasonyeza mikhalidwe yaumulungu. Pakati pa amenewa, Mulungu wasankhapo chiŵerengero chochepa kukalamulira monga mafumu ndi Kristu kumwamba. Amenewa amanenedwa kukhala “ana” kapena ‘ana ake aamuna.’ Kaamba ka maumboni owonjezereka, wonani mutu wankhani waukulu wakuti “Kubadwanso.”)

Aroma 8:19-21, NW: “Chiyembekezo chaphamphu cha chilengedwe chikuyembekezera kuvumbulutsidwa kwa ana a Mulungu . . . Chilengedwe chinichenicho chidzamasulidwanso kuukapolo wachivundi ndi kukhala ndi ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.” (Mpumulo wa anthu udzadza pamene “ana a Mulungu,” atalandira moyo wakumwamba, ‘abvumbulitsidwa’ kukhala ochitira anthu kachitidwe kotsimikizirika motsogozedwa ndi Kristu. Okhulupirikawo padziko lapansi [otchulidwa kukhala “chilengedwe” m’lemba iri] atafikira ungwiro waumuthu nasonyeza kukhulupirika kosagwedera kwa Yehova monga Mfumu ya Chilengedwe chonse, pamenepo nawonso adzakhala ndi unansi wabwino wa ana a Mulungu. Anthu amafuko onse nawonso adzakhala nawo.)

Kodi anthu amafuko onse adzagwirizanitsidwadi monga abale ndi alongo?

Kwa awo amene anali ophunzira ake owona, Yesu anati: “Inu nonse muli abale.” (Mat. 23:8) Pambuyo pake anawonjezera kuti: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.”—Yoh. 13:35.

Mosasamala kanthu za kupanda ungwiro kwaumunthu, lingaliro laumodzi limenelo linali lotsimikizirika pakati pa Akristu oyambirira. Mtumwi Paulo adalemba kuti: “Muno mulibe Myuda kapena Mhelene, muno mulibe kapolo, kapena mfulu, muno mulibe mwamuna kapena mkazi; pakuti muli nonse mmodzi mwa Kristu Yesu.”—Agal. 3:28.

Ubale Wachikristu wosadodometsedwa ndi ufuko ukupezeka pakati pa Mboni za Yehova m’zaka za zana la 20. Wolemba nkhani William Whalen anati mu U.S. Catholic: “Ndikhulupirira kuti umodzi wa mikhalidwe yokondweretsa koposa ya [gulu la Mboni za Yehova] wakhala mchitidwe wake wozoloŵereka wa kufanana kwa mafuko.” Pambuyo pakuchita mafufuzidwe aakulu pa Mboni za Yehova mu Afirika, katswiri wa zamakhalidwe aanthu pa Yunivesite ya Oxford Bryan Wilson anafotokoza kuti: “Mwinamwake Mboni ziri ndi chipambano kuposa kagulu kena kali konse m’liŵiro limene zikuthetsera kusankhana mafuko pakati pa ziŵalo zawo zatsopano.” Posimba za msonkhano wamitundu yonse wa Mboni zochokera kumaiko 123, The New York Times Magazine inati: “Mboni zinachititsa chidwi nzika za New York osati kokha ndi ziŵerengero zawo, koma ndi kusiyanasiyana kwawoko (iwo anaphatikizamo anthu ochokera m’mikhalidwe yonse), khalidwe lawo lakusaŵerengera fuko (Mboni zochuluka ndizo Anegro) ndi kudzisungira kwawo kwachete ndi kwadongosolo.”

Mwamsanga Ufumu wa Mulungu udzawononga dongosolo liripoli la zinthu lopanda umulungu, kuphatikizapo onse amene alibe chikondi chenicheni kwa onse aŵiri Yehova Mulungu ndi anthu anzawo. (Dan. 2:44; Luka 10:25-28) Mawu a Mulungu amalonjeza kuti opulumukawo adzakhala anthu “ochokera ku mitundu yonse ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.” (Chiv. 7:9) Atagwirizanitsidwa pamodzi ndi kulambiridwa kwa Mulungu wowona mwa chikhulupiriro mwa Yesu Kristu, ndi mwa kukondana wina ndi mnzake, iwo adzapangadi banja laumuthu logwirizana.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena