-
Ndandanda ya Mlungu wa September 28Utumiki wa Ufumu—2015 | September
-
-
Ndandanda ya Mlungu wa September 28
MLUNGU WOYAMBIRA SEPTEMBER 28
Nyimbo Na. 99 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 19 ndime 9-17 (30 min.)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 2 Mafumu 23-25 (8 min.)
Na. 1: 2 Mafumu 23:8-15 (Osapitirira 3 min.)
Na. 2: Zimene Angelo Amachita Pokwaniritsa Cholinga cha Mulungu—bh tsa. 97-98 ndime 4-6 (5 min.)
Na. 3: Tumikirani Yehova Mokhulupirika—bh tsa. 144-145 ndime 1-4 (5 min.)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezi Uno: ‘Muzichitira umboni mokwanira za uthenga wabwino.’—Mac. 20:24.
10 min: Paulo ndi Anzake Anachitira Umboni Mokwanira ku Filipi. Nkhani yokambirana. Werengani Machitidwe 16:11-15. Kenako kambiranani mmene mavesi amenewa angatithandizire mu utumiki.
20 min: “Tizigwiritsa Ntchito Kabuku ka Uthenga Wabwino Pophunzitsa Anthu.” Mafunso ndi mayankho. Mukamaliza kukambirana ndime 3, chitani chitsanzo chokonzekeredwa bwino chosonyeza wofalitsa akugawira kabuku ka Uthenga Wabwino n’kukambirana ndi munthuyo ndime imodzi.
Nyimbo Na. 114 ndi Pemphero
-
-
Tizigwiritsa Ntchito Kabuku ka Uthenga Wabwino Pophunzitsa AnthuUtumiki wa Ufumu—2015 | September
-
-
1. Kodi kabuku ka Uthenga Wabwino kanalembedwa bwanji?
1 Utumiki wa Ufumu wa July chaka chino, unanena kuti kabuku ka Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu ndi kamodzi mwa zinthu zimene timagwiritsa ntchito kwambiri pophunzitsa anthu Mawu a Mulungu. Malemba amene ali m’kabukuka sanawagwire mawu, n’cholinga choti munthu amene tikuphunzira naye kabukuka azimva malembawa kuchokera m’Baibulo. Mabuku athu ambiri amalembedwa moti munthu azitha kuwerenga yekha n’kumvetsa uthenga wake. Koma kabuku ka Uthenga wabwino anakalemba m’njira yoti tizikambirana ndi munthu amene akufuna kuphunzira choonadi kuti akamvetse. Choncho tikamagawira kabukuka, tiziyesetsa kusonyeza munthu mmene timaphunzirira, n’cholinga choti aone kuti kuphunzira mfundo za m’Baibulo n’kosangalatsa.—Mat. 13:44.
-