Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb16 May tsamba 2
  • Kodi Mumagwiritsa Ntchito Laibulale ya JW?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumagwiritsa Ntchito Laibulale ya JW?
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
  • Nkhani Yofanana
  • Laibulale Yokwanira M’dzanja Limodzi
    Kodi Zopereka Zanu Zimagwiritsidwa Ntchito Bwanji?
  • Mmene Tingagwiritsire Ntchito Laibulale ya JW
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
  • Kachipangizo Kothandiza Kwambiri
    Kodi Zopereka Zanu Zimagwiritsidwa Ntchito Bwanji?
  • Kodi Laibulale ya pa Nyumba ya Ufumu Ingatithandize Bwanji?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
mwb16 May tsamba 2

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Mumagwiritsa Ntchito Laibulale ya JW?

Laibulale ya JW ndi yaulere ndipo ingakuthandizeni kupanga dawunilodi zinthu monga Baibulo, magazini, mavidiyo ndi zinthu zina zongomvetsera kuti muzizigwiritsa ntchito mufoni, tabuleti kapena pakompyuta.

Mabuku a m’Baibulo ali pa Laibulale ya JW

KODI MUNGAIPEZE BWANJI?: Pitani pa Intaneti pamalo amene pamapezeka pulogalamu yopangira dawunilodi mapulogalamu osiyanasiyana. Kenako mungapange dawunilodi Laibulale ya JW, n’kuisunga m’chipangizo chanu. Mukatero tsegulani pulogalamuyi ndi kupanga dawunilodi mabuku kapenanso zinthu zina zomwe mukufuna. Ngati kunyumba kwanu kulibe netiweki ya intaneti, mukhoza kupita ku Nyumba ya Ufumu, kunyumba kwa mnzanu, kapenanso mungakalipire kumalo ena kumene kuli netiweki ya intaneti m’dera lanu. Mukapanga dawunilodi mabuku n’kuwasunga m’chipangizo chanu, simufunikiranso kupita pa intaneti kuti muwawerenge. Komabe popeza kuti nthawi ndi nthawi papulogalamuyi amaikapo zinthu zina zatsopano, muyenera kumapita pa intaneti kuti muone zomwe aikapo.

KODI INGAKUTHANDIZENI BWANJI? Mungathe kugwiritsa ntchito Laibulale ya JW pophunzira Baibulo panokha komanso pamisonkhano yampingo. Ndi yothandizanso kwambiri mu utumiki makamaka polalikira mwamwayi ngakhale kwa anthu omwe safuna kuwalalikira.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena