CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 87-91
Pitirizani Kukhala M’malo Otetezeka a Wam’mwambamwamba
Timatetezeka mwauzimu tikakhala “m’malo achitetezo” a Yehova
Kuti tikhale m’malo achitetezo a Yehova, timafunika kudzipereka komanso kubatizidwa
Anthu amene sakhulupirira Mulungu sadziwa malo amenewa
Anthu amene ali m’malo achitetezo a Yehova sakopeka ndi anthu kapena chilichonse chimene chingapangitse kuti asiye kukhulupirira komanso kukonda Mulungu
“Wosaka mbalame” akufunitsitsa kutigwira
Mbalame ndi zochenjera kwambiri, ndipo ndi zovuta kugwira
Wosaka mbalame amayang’anitsitsa zimene mbalamezo zimakonda, ndipo amakonza misampha kuti azigwire
Nayenso Satana, yemwe ndi “wosaka mbalame,” amayang’anitsitsa zimene atumiki a Yehova amakonda kuchita ndipo amatchera misampha n’cholinga choti awagwire
Misampha 4 yoopsa imene Satana amagwiritsa ntchito kuti atikole:
Kuopa Anthu
Kukonda Chuma
Zosangalatsa Zosayenera
Kusemphana Maganizo ndi Anthu Ena