Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp20 No. 3 tsamba 11
  • Anthu Amene Amamvera Mulungu Amalandira Madalitso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anthu Amene Amamvera Mulungu Amalandira Madalitso
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2020
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • 1. TIKAMAMVERA MULUNGU TIMAKHALA ANZERU
  • 2. TIKAMAMVERA MULUNGU TIMAKHALA OSANGALALA
  • Chikondi Cha Mulungu Sichimatha
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
  • Zimene “Kukonda Mulungu Kumatanthauza”
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
  • Kodi Ndinu ‘Okonzeka Kumvera’?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Kodi Yehova Amafuna Kuti Tizichita Chiyani?
    Nsanja ya Olonda—2009
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2020
wp20 No. 3 tsamba 11
Banja likucheza mosangalala. Mayi akukonza chakudya limodzi ndi mwana wake wina. Bambo akuona buku la zithunzi limodzi ndi mwana wina pabalaza.

Tikamamvera malamulo a Mulungu timakhala ndi moyo wosangalala

Anthu Amene Amamvera Mulungu Amalandira Madalitso

Mneneri Mose ananena kuti tikamamvera malamulo a Mulungu, iye adzatidalitsa. (Deuteronomo 10:13; 11:27) Tizimvera Mulungu chifukwa chomukonda osati chifukwa choopa chilango. Makhalidwe abwino a Mulungu amatichititsa kuti tizimumvera ndi kuyesetsa kupewa zimene zingamukhumudwitse. Zili choncho “chifukwa kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake.”​—1 Yohane 5:3.

Kodi Mulungu amatidalitsa bwanji tikamamumvera? Taganizirani njira ziwiri izi.

1. TIKAMAMVERA MULUNGU TIMAKHALA ANZERU

“Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino, . . . ndimakuchititsani kuti muyende m’njira imene muyenera kuyendamo.”​—YESAYA 48:17.

Yehova Mulungu, yemwe ndi Mlengi wathu, amatidziwa bwino ndipo amatipatsa malangizo amene angatithandize. Kuti zimene tikuphunzira zitithandize kusankha zinthu mwanzeru, tiyenera kuphunzira zimene Mulungu amafuna m’Malemba Opatulika komanso kuchita zimene tikuphunzirazo.

2. TIKAMAMVERA MULUNGU TIMAKHALA OSANGALALA

“Odala ndi amene akumva mawu a Mulungu ndi kuwasunga!”​—LUKA 11:28.

Masiku ano anthu mamiliyoni ambiri amene amamvera Mawu a Mulungu amakhala ndi moyo wosangalala. Mwachitsanzo, taganizirani bambo wina wa ku Spain amene sankachedwa kupsa mtima ndipo ankachitira nkhanza anthu ena kuphatikizapo mkazi wake. Tsiku lina anawerenga zimene mneneri Mose analemba zokhudza Yosefe, mwana wa Yakobo, yemwe anali wougwira mtima. Yosefe anagulitsidwa ngati kapolo komanso anaikidwa m’ndende ngakhale kuti sanalakwe. Komabe iye anakhalabe wougwira mtima, ankachita zinthu mwamtendere komanso ankakhululukira ena. (Genesis, machaputala 37-45) Bambo wa ku Spain uja anati: “Kuganizira chitsanzo cha Yosefe kunandithandiza kuti nanenso ndikhale wougwira mtima, ndizichita zinthu mokoma mtima ndi ena komanso ndikhale wodziletsa. Zimenezi zathandiza kuti panopa ndizikhala moyo wosangalala.”

M’Malemba Opatulika muli malangizo enanso okhudza mmene tingamachitire zinthu ndi anthu ena. Tiyeni tione mfundo zina m’nkhani yotsatirayi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena