Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp20 No. 3 tsamba 12
  • Kodi Tingasonyeze Bwanji Kuti Timakonda Anzathu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Tingasonyeze Bwanji Kuti Timakonda Anzathu?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2020
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ZIMENE MALEMBA OPATULIKA AMANENA PA NKHANI YA CHIKONDI
  • ZIMENE KUKONDA ANZATHU KUMATANTHAUZA
  • “Pitirizani Kusonyeza Chikondi”
    Yandikirani Yehova
  • Chikondi (Agape)—Zimene Sichili ndi ZImene Chili
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Chikondi Ndi Khalidwe Lamtengo Wapatali Kwambiri
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Kodi Tingatani Kuti Tizikondana Kwambiri?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2020
wp20 No. 3 tsamba 12
Msamariya wachifundo wa m’fanizo la Yesu akupaka mafuta pabala la munthu amene anamenyedwa n’kusiyidwa m’mbali mwa msewu.

Chikondi chimatichititsa kuti tiziika zofuna za ena pamalo oyamba

Kodi Tingasonyeze Bwanji Kuti Timakonda Anzathu?

Popeza kuti tinachokera kwa munthu mmodzi Adamu, tonse ndife banja limodzi. Ngakhale kuti anthu a m’banja limodzi amayenera kukondana komanso kulemekezana, masiku ano anthu sasonyezana chikondi choterechi. Mlengi wathu wachikondi safuna zimenezi.

ZIMENE MALEMBA OPATULIKA AMANENA PA NKHANI YA CHIKONDI

“Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.”​—LEVITIKO 19:18.

“Pitirizani kukonda adani anu.”—MATEYU 5:44.

ZIMENE KUKONDA ANZATHU KUMATANTHAUZA

Onani mmene Mulungu anafotokozera chikondi m’Mawu ake opezeka pa 1 Akorinto 13:4-7:

“Chikondi n’choleza mtima ndiponso n’chokoma mtima.”

Taganizirani izi: Kodi mumamva bwanji anthu ena akamakuchitirani zinthu moleza mtima ndiponso mokoma mtima komanso ngati samakulusirani mukalakwitsa zinazake?

“Chikondi sichichita nsanje.”

Taganizirani izi: Kodi mumamva bwanji ngati anthu ena amangokukayikirani zilizonse kapena kukuchitirani nsanje?

Chikondi “sichisamala zofuna zake zokha.”

Taganizirani izi: Kodi mumamva bwanji ngati anthu ena amalemekeza maganizo anu ndipo samangokakamira maganizo awo okha?

Chikondi “sichisunga zifukwa.”

Taganizirani izi: Mulungu ndi wofunitsitsa kukhululukira anthu omwe achimwa n’kulapa. “Iye sadzakhalira kutiimba mlandu nthawi zonse chifukwa cha zolakwa zathu, kapena kutisungira mkwiyo mpaka kalekale.” (Salimo 103:9) Anthufe timasangala ngati munthu amene tamulakwira watikhululukira. Nafenso tizikhala okonzeka kukhululukira anthu amene atilakwira.​—Salimo 86:5.

Chikondi “sichikondwera ndi zosalungama.”

Taganizirani izi: Tikakumana ndi vuto linalake sitimafuna kuti anthu ena azisangalala. Choncho nafenso sitiyenera kusangalala anthu ena akakumana ndi mavuto, ngakhale kuti anthuwo sanatichitire zabwino.

Kuti Mulungu azitidalitsa, tiyenera kukonda ena posatengera msinkhu wawo, dziko limene akuchokera komanso chipembedzo chawo. Njira imodzi imene tingasonyezere chikondichi ndi kuthandiza ena.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena