Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp20 No. 3 tsamba 13
  • Anthu Amene Amathandiza Ena Amalandira Madalitso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anthu Amene Amathandiza Ena Amalandira Madalitso
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2020
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ZIMENE MALEMBA OPATULIKA AMANENA
  • ZIMENE KUTHANDIZA ENA KUMATANTHAUZA
  • Kodi Kukhala “Msamariya Wachifundo” Kumatanthauza Chiyani?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kodi Mumalola Kuti Yehova Akuthandizeni?
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Kodi Tsankho Lingathe Bwanji?
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Kodi Ndinu “Wolemera kwa Mulungu”?
    Nsanja ya Olonda—2007
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2020
wp20 No. 3 tsamba 13
Munthu akusonyeza mnzake njira pogwiritsa ntchito mapu.

Kodi mukhoza kuthandiza ena posatengera msinkhu wawo, dziko limene akuchokera kapena chipembedzo chawo?

Anthu Amene Amathandiza Ena Amalandira Madalitso

Padziko lonse anthu ambiri amasowa chakudya ndi pokhala. Ena ali ndi zinthu zimenezi koma amasowa chiyembekezo chabwino chokhudza tsogolo lawo. Mulungu amafuna kuti tizithandiza anthu oterewa ndipo adzatidalitsa tikamachita zimenezi.

ZIMENE MALEMBA OPATULIKA AMANENA

“Wokomera mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova, ndipo adzam’bwezera zimene anachitazo.”​—MIYAMBO 19:17.

ZIMENE KUTHANDIZA ENA KUMATANTHAUZA

Yesu anafotokoza nkhani yokhudza munthu amene achifwamba anamuvulaza n’kumusiya atatsala pang’ono kufa. (Luka 10:29-37) Munthu wina wachifundo yemwe sankadziwana ndi munthu wovulazidwayo anaima n’kumuthandiza. Iye anachita zimenezi ngakhale kuti anali osiyana mitundu.

Kuwonjezera pa kutsuka mabala a munthu wovulala ndi kumupatsa zinthu zina zofunikira, munthu wachifundoyu analimbikitsa ndi kutonthoza wovulalayo ndipo zimenezi zinamuthandiza kuti asakhalenso ndi nkhawa.

Kodi nkhaniyi ikutiphunzitsa chiyani? Yesu anatiphunzitsa kuti tiziyesetsa kuchita zimene tingakwanitse pothandiza ena. (Miyambo 14:31) Malemba Opatulika amatiuza kuti posachedwapa Mulungu adzathetsa umphawi ndi kuvutika. Komabe mwina tingadzifunse kuti, Kodi Mulungu adzachita liti zimenezi nanga adzazichita bwanji? Nkhani yotsatirayi ifotokoza madalitso amene Mlengi wanu wachikondi wakulonjezani.

“MULUNGU SANANDITAYEPO”!

Yofotokozedwa ndi bambo wina wochokera ku Gambia

“Nditafika ku Europe, ndinalibe chilichonse. Sindinali pa ntchito, ndinalibe ndalama ngakhalenso nyumba. Zimene ndaphunzira m’Malemba Opatulika zandithandiza kuti ndizigwira ntchito mwakhama ndi kuthandiza ena m’malo mongodalira kuti anthu ena azindithandiza. Mulungu sananditayepo ndipo wakhala akundithandiza nthawi zonse!”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena