Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp20 No. 3 tsamba 4-5
  • Mlengi Wathu Wachikondi Amatisamalira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mlengi Wathu Wachikondi Amatisamalira
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2020
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • 1. MLENGI WATHU AMAWALITSA DZUWA
  • 2. MLENGI WATHU AMAVUMBITSA MVULA
  • 3. MLENGI WATHU AMATIPATSA CHAKUDYA NDI ZOVALA
  • Tizithokoza Mulungu Chifukwa cha Mvula
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Muzifunafuna Ufumu Osati Zinthu Zina
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Dziŵani Mlengi Wanu
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Uyo Amene Anapanga Zinthu Zonse
    Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2020
wp20 No. 3 tsamba 4-5
Dzuwa likutuluka pamwamba pa mapiri.

Mlengi Wathu Wachikondi Amatisamalira

1. MLENGI WATHU AMAWALITSA DZUWA

Kodi moyo ukanakhala bwanji padzikoli zikanakhala kuti kulibe dzuwa? Mphamvu ya dzuwa imathandiza kuti mitengo itulutse masamba, maluwa, zipatso ndi njere. Imathandizanso kuti mizu ya mitengo izitha kutenga madzi kuchokera munthaka n’kuwapititsa m’masamba ndipo kenako madziwo akapita mumpweya amakhala nthunzi.

Minda ya tiyi yomwe ili m’mbali mwa phiri.

2. MLENGI WATHU AMAVUMBITSA MVULA

Mvula ndi mphatso yamtengo wapatali imene Mulungu amatipatsa ndipo imathandiza kuti dziko lapansi lizitulutsa chakudya chimene anthufe timadya. Mulungu amatipatsa mvula kuchokera kumwamba ndi nyengo zimene zokolola zathu zimakhala zambiri, amadzadza mitima yathu ndi chakudya komanso chimwemwe.

Mbalame yakhala panthambi ndipo ikuyesetsa kuwakha kachipatso kamene kakugwa.

3. MLENGI WATHU AMATIPATSA CHAKUDYA NDI ZOVALA

Abambo ambiri amadera nkhawa za mmene angapezere banja lawo chakudya chokwanira ndiponso zovala. Taonani zimene Malemba amanena: “Onetsetsani mbalame zam’mlengalenga, pajatu sizifesa mbewu kapena kukolola, kapenanso kusunga chakudya m’nkhokwe. Koma Atate wanu wakumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengo wapatali kuposa mbalame kodi?”​—Mateyu 6:25, 26.

“Phunzirani pa mmene maluwa akutchire amakulira. . . . Komatu ndikukuuzani kuti ngakhale [Mfumu] Solomo mu ulemerero wake wonse sanavalepo zokongola ngati lililonse la maluwa amenewa. Tsopano ngati Mulungu amaveka chotero zomera zakutchire, . . .  kodi iye sadzakuvekani kuposa pamenepo?”​—Mateyu 6:28-30.

Popeza kuti Mulungu amatha kutipatsa chakudya ndi zovala, n’zosakayikitsa kuti angatithandizenso kupeza zinthu zina zofunikira pa moyo. Tikamafunitsitsa kuchita zimene Mulungu amafuna, iye angadalitse khama lathu ndipo tingalime n’kupeza chakudya kapena angatithandize kupeza ntchito kuti tizigula zinthu zomwe tikufunikira.—Mateyu 6:32, 33.

Zoonadi, tili ndi zifukwa zabwino zotichititsa kukonda Mulungu tikaganizira zomwe analenga monga dzuwa, mvula, mbalame komanso maluwa. Nkhani yotsatirayi itithandiza kudziwa mmene Mlengi wathu wathandizira anthu kudziwa malonjezo ake.

Mlengi wathu ‘amawalitsa dzuwa ndi kuvumbitsa mvula.’​—MATEYU 5:45

Mlengi wathu amatikonda kwambiri komanso amatisamalira. Mofanana ndi bambo wachikondi, Mulungu amasamalira banja lake. Malemba Opatulika amafotokoza kuti Mulungu amapereka zinthu mowolowa manja ndipo “amadziwa zimene mukufuna musanapemphe n’komwe.”​—Mateyu 6:8.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena