CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YEREMIYA 51–52
Nthawi Zonse Mawu a Yehova Amakwaniritsidwa
Yehova ananeneratu molondola zinthu zam’tsogolo
Msilikali wachiperisiya
“Nolani mivi yanu”
Amedi ndi Aperisi anali akatswiri oponya mivi ndipo ankadalira kwambiri mauta. Iwo ankanola mivi yawo kuti akabaya izilowa mkati kwambiri
“Amuna amphamvu a ku Babulo asiya kumenya nkhondo”
Mbiri ya Nabonidus imati: “Magulu a nkhondo a Koresi analowa m’Babulo popanda kumenya nkhondo.” Izi zikutanthauza kuti Koresi analowa mumzinda wa Babulo popanda wolimbana naye ndipo n’zogwirizana ndi zimene ulosi wa Yeremiya unanena
Mbiri ya Nabonidus
“Babulo adzakhala milu yamiyala [ndiponso] bwinja mpaka kalekale”
Kuyambira m’chaka cha 539 B.C.E., ulemerero wa Babulo unayamba kuchepa. Alekizanda Wamkulu ankafuna kuti mzinda wa Babulo ukhale likulu la ulamuliro wake, koma pasanapite nthawi anamwalira. Chikhristu chitangoyamba kumene, mtumwi Petulo ankafika ku Babulo chifukwa kunali Ayuda ena omwe ankakhala kumeneko. Koma pofika m’zaka za m’ma 300 C.E., mzindawo unawonongedwa ndipo sunakhaleponso