CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | ZEKARIYA 1-8
“Gwirani Chovala cha Munthu Amene ndi Myuda”
Amuna 10 ochokera m’zilankhulo zonse za anthu a mitundu ina, adzagwira chovala cha munthu amene ndi Myuda ndi kunena kuti: “Anthu inu tipita nanu limodzi.” M’masiku otsiriza ano, anthu a mitundu yonse akubwera kudzalambira Yehova limodzi ndi Akhristu odzozedwa
Kodi a nkhosa zina amathandiza Akhristu odzozedwa m’njira ziti masiku ano?
Amagwira nawo ntchito yolalikira ndi mtima wonse
Amathandiza ntchito yolalikira ndi ndalama zawo