CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | ZEKARIYA 9-14
Musachoke ‘M’chigwa cha Pakati pa Mapiri’
Yehova anapanga “chigwa chachikulu kwambiri” mu 1914 pamene anakhazikitsa Ufumu wa Mesiya, womwe uli ngati “phiri” locheperapo poyerekezera ndi ulamuliro wake wachilengedwe chonse. Kuyambira mu 1919, atumiki a Mulungu akhala ali wotetezeka ‘m’chigwa cha pakati pa mapiri’ chimenechi.
Kodi anthu amathawira bwanji “kuchigwa” cha chitetezo?
Aliyense amene ali kunja kwa chigwa chophiphiritsachi adzawonongedwa pa nkhondo ya Aramagedo
Kodi ndingatani kuti ndikhalebe m’chigwa cha chitetezo