Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb18 March tsamba 8
  • Kodi Tingasonyeze Bwanji Kuti Timakonda Mulungu Komanso Anzathu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Tingasonyeze Bwanji Kuti Timakonda Mulungu Komanso Anzathu?
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • Nkhani Yofanana
  • Kupindula ndi Kuŵerenga Baibulo Tsiku ndi Tsiku
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Kondwerani ndi Mawu a Mulungu
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Mmene Tingaŵerengere ndi Kukumbukira
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Zimene Tingachite Kuti Tizipindula Kwambiri Tikamawerenga Baibulo
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
mwb18 March tsamba 8

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Tingasonyeze Bwanji Kuti Timakonda Mulungu Komanso Anzathu?

Ngakhale kuti Akhristu satsatira Chilamulo cha Mose, malamulo ake awiri aakulu kwambiri omwe ndi kukonda Mulungu komanso anzathu, amasonyezabe zimene Yehova amafuna kuti tizichita. (Mat. 22:37-39) Chikondi chimenechi sichimangoyamba chokha mwa munthu. Timafunika kuchikulitsa. Ndiye tingachite bwanji zimenezi? Njira yofunika kwambiri imene tingachitire zimenezi ndi kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku. Tikamaphunzira zimene Malemba amanena zokhudza makhalidwe a Mulungu, timayamba kuona “ubwino wa Yehova.” (Sal. 27:4) Izi zimachititsa kuti tiyambe kumukonda kwambiri komanso timayamba kuganiza mofanana naye. Zimenezi zimatilimbikitsa kutsatira malamulo ake, kuphatikizapo lamulo losonyeza ena chikondi chopanda dyera. (Yoh. 13:34, 35; 1 Yoh. 5:3) Tsopano onani mfundo zitatu zomwe zingatithandize kuti tizisangalala kwambiri tikamawerenga Baibulo.

  • Muziyerekezera kuti mukumva komanso kuona zimene zikuchitikazo m’maganizo mwanu. Muziyerekezera kuti munalipo pa nthawiyo. Kodi mukuona komanso kumva chiyani, nanga pamalopo pakumveka kafungo kotani? Kodi anthu omwe ali pamalowo akumva bwanji?

    M’bale akuyerekezera kuti akuona zimene wawerenga m’Baibulo
  • Muzisinthasintha njira zowerengera. Mungagwiritse ntchito njira ngati izi: Mungamawerenge mokweza kapena kumatsatira pamene mukumvetsera Baibulo longomvetsera. Mungamawerenge zokhudza munthu winawake wotchulidwa m’Baibulo kapena mfundo zokhudza nkhani inayake m’malo mowerenga machaputala motsatira ndondomeko yake. Mwachitsanzo, mungagwiritse ntchito Kabuku Kothandiza Kuphunzira Mawu a Mulungu mutu 4 kapena 16 kuti muwerenge nkhani zokhudza Yesu. Mungamawerenge chaputala chonse chomwe pachokera lemba la tsiku limenelo. Mukhozanso kumawerenga Baibulo motsatira nthawi imene mabuku ake analembedwa.

    Mlongo akuwerenga Baibulo pa jw.org
  • Muziwerenga n’cholinga choti mumvetse. Kuwerenga chaputala chimodzi pa tsiku n’cholinga choti mumvetse komanso kusinkhasinkha zimene mukuwerengazo n’kopindulitsa kwambiri, kusiyana ndi kuwerenga machaputala ambirimbiri n’cholinga choti mumalize kuwerenga Baibulo lonse. Muziganizira malo amene nkhaniyo inachitikira komanso mbali zosiyanasiyana za nkhaniyo. Mukhozanso kugwiritsa ntchito mapu ndiponso malifalensi omwe ali mu danga la pakati m’Baibulo lanu. Mungachitenso bwino kumafufuza mfundo zomwe simunazimvetse. Ngati n’zotheka, muzisinkhasinkha zimene mwawerengazo kwa nthawi yofanana ndi imene mwawerenga Baibulo.

    Zithunzi ziwiri zosonyeza zakumapeto za m’Baibulo la Dziko Latsopano
    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena