MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Muzisamala Mukamacheza ndi Anzanu pa Intaneti
N’CHIFUKWA CHIYANI M’POFUNIKA KUSAMALA? Monga mmene zilili ndi zipangizo zambiri zomwe zingakuthandizeni kapena kukuvulazani, malo ochezera a pa intaneti angakhale abwino kapena oipa malinga ndi mmene tikuwagwiritsira ntchito. Akhristu ena amasankha kusagwiritsa ntchito malo amenewa. Pomwe ena amagwiritsa ntchito malowa pocheza komanso kulankhulana ndi achibale ndiponso anzawo. Koma Satana amafuna kuti tizigwiritsa ntchito malowa molakwika ndipo zimenezi zingaipitse mbiri ya munthu komanso zingawononge ubwenzi wake ndi Yehova. Mofanana ndi Yesu, nafenso tikhoza kugwiritsa ntchito mfundo za m’Mawu a Mulungu kuti tizindikire mayesero komanso kuwapewa.—Luka 4:4, 8, 12.
ZINTHU ZIMENE MUYENERA KUSAMALA NAZO:
Kutha nthawi yaitali mukucheza pa intaneti. Tikamathera nthawi yambiri tikucheza ndi anthu pa intaneti, tingamalephere kuchita zinthu zomwe zingalimbitse ubwenzi wathu ndi Yehova
Mfundo za m’Baibulo: Aef. 5:15, 16; Afil. 1:10
Kuona kapena kuwerenga zinthu zoipa. Kuona zithunzi zosonyeza anthu atavala mosayenera kungachititse kuti munthu ayambe kuonera zolaula kapena kuchita chiwerewere. Kuwerenga mabuku kapena nkhani zimene anthu ampatuko amalemba pa intaneti kungawononge chikhulupiriro chathu
Mfundo za m’Baibulo: Mat. 5:28; Afil. 4:8
Kuika zithunzi zosayenera komanso kulemba makomenti oipa. Popeza mtima ndi wonyenga, munthu akhoza kuika zithunzi zosayenera kapena kulemba makomenti oipa pamalo ochezera a pa intaneti. Koma zimenezi zikhoza kuwononga mbiri ya munthu komanso zingachititse kuti asokoneze ubwenzi wake ndi Yehova
Mfundo za m’Baibulo: Aroma 14:13; Aef. 4:29
ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZICHITA ZINTHU MWANZERU MUKAMACHEZA NDI ANZANU PA INTANETI, KENAKO ONANI MMENE MUNGAPEWERE MAVUTO OMWE AKUSONYEZEDWA M’ZITHUNZIZI: