Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb22 March tsamba 9
  • Kodi Mumacheza ndi Ndani pa Intaneti?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumacheza ndi Ndani pa Intaneti?
  • Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ndi Bwino Kucheza pa Intaneti?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • Muzisamala Mukamacheza ndi Anzanu pa Intaneti
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • Kodi ndiyenera kudziwa zotani zokhudza malo ochezera a pa Intaneti?—Gawo 2
    Galamukani!—2011
  • Ana Akamagwiritsa Ntchito Intaneti Zimene Makolo Ayenera Kudziwa
    Galamukani!—2008
Onani Zambiri
Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
mwb22 March tsamba 9

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Mumacheza ndi Ndani pa Intaneti?

Mawu akuti mnzako amatanthauza “munthu amene umagwirizana naye chifukwa choti mumakondana kapena kulemekezana.” Mwachitsanzo, Yonatani ndi Davide anakhala pa ubwenzi wolimba kwambiri kungochokera pamene Davide anapha Goliyati. (1Sa 18:1) Aliyense anasonyeza makhalidwe amene anachititsa kuti mnzake ayambe kumukonda. Choncho kuti munthu ukhale pa ubwenzi wolimba ndi munthu wina, zimadalira ngati ukumudziwadi molondola. Kuti umudziwe bwino munthu wina pamafunika nthawi komanso khama. Komabe, pa malo ochezera a pa intaneti munthu ukhoza kukhala ndi “anzako” mwa kungodina batani. Chifukwa choti anthu pa intaneti akhoza kupanga pulani ya zimene angalembe komanso akhoza kubisa kuti ena asaone zinthu zina zokhudza iwowo, kumakhala kovuta kudziwa makhalidwe awo enieni. Choncho tiyenera kuganizira mosamala tisanavomere anthu oti tizicheza nawo pa intaneti. Ngati munthu wina amene simukumudziwa akufuna kuti mukhale mnzake pa intaneti, musamachite mantha kukana poopa kuti mumukhumudwitsa. Chifukwa choopa zimene zingachitike, anthu ena anasankha kuti asamagwiritse ntchito n’komwe malo ochezera a pa intaneti. Komabe, ngati mwasankha kugwiritsa ntchito malowa, kodi muyenera kukumbukira chiyani?

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZICHITA ZINTHU MOSAMALA MUKAMACHEZA NDI ANZANU PA INTANETI, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Muzichita Zinthu Mosamala Mukamacheza ndi Anzanu pa Intaneti.” Mtsikana akuyang’ana modabwa zithunzi zake zimene zaikidwa pa TV.

    Kodi muyenera kuganizira chiyani musanaike zithunzi kapena musanalembe ndemanga pa malo ochezera a pa intaneti?

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Muzichita Zinthu Mosamala Mukamacheza ndi Anzanu pa Intaneti.” Pa sikelo pali chithunzi chokongola cha mtsikana, ndipo mbali ina ya sikeloyo kuli ndalama za siliva. Chithunzicho chikulemera kuposa ndalamazo.

    N’chifukwa chiyani muyenera kusankha mosamala anzanu ocheza nawo pa intaneti?

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti ‘Muzichita Zinthu Mosamala Mukamacheza ndi Anzanu pa Intaneti.’ Azibambo awiri ooneka moopsa akuonetsa mnyamata positi ya pamalo ochezera a pa intaneti ndipo mnyamatayo watseka maso ake.

    N’chifukwa chiyani muyenera kudziikira malire pa nthawi imene mumathera mukucheza ndi anzanu pa intaneti?—Aef 5:15, 16

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena