Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb18 September tsamba 4
  • Muzitsatira Yesu Muli ndi Zolinga Zabwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzitsatira Yesu Muli ndi Zolinga Zabwino
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • Nkhani Yofanana
  • Okonda Chilungamo Palibe Chowakhumudwitsa
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • Kodi Mudzakhumudwa N’kusiya Kutsatira Yesu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • “Chirimikani”—Musakhumudwe
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Tizipewa Kuchita Zinthu Zimene Zingakhumudwitse Ena
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
mwb18 September tsamba 4

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOHANE 5-6

Muzitsatira Yesu Muli ndi Zolinga Zabwino

6:9-11, 25-27, 54, 66-69

Yesu atanena fanizo lomwe linasokoneza mitu ophunzira ake, ambiri anakhumudwa ndipo anasiya kumutsatira. Panali patangodutsa tsiku limodzi kuchokera pamene Yesu anadyetsa khamu la anthu mozizwitsa, ndipo izi zinkatsimikizira kuti anali ndi mphamvu zochokera kwa Mulungu. Ndiyeno n’chifukwa chiyani anthuwo anakhumudwa? N’zoonekeratu kuti iwo ankamutsatira ndi zolinga zadyera. Ankangofuna kuti Yesu aziwapatsa zakudya.

Aliyense ayenera kudzifunsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani ndimatsatira Yesu? Kodi ndimamutsatira chifukwa cha madalitso amene ndikupeza panopa komanso amene ndidzapeze m’tsogolo basi? Kapena n’chifukwa choti ndimakonda Yehova ndipo ndimafuna kuchita zimene amafuna?’

Yesu anadyetsa ophunzira ake mozizwitsa; ophunzira ambiri anasiya kumutsatira ndipo Yesu anafunsa atumwi ake ngati nawonso akufuna kumusiya

N’chifukwa chiyani zili zosavuta kuti tikhumudwe ngati timangotumikira Yehova pa zifukwa zotsatirazi?

  • Timasangalala kukhala pakati pa anthu a Yehova

  • Tikufuna kudzakhala m’Paradaiso

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena