Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb18 September tsamba 7
  • Muzitsanzira Khristu pa Nkhani Yokhala Odzichepetsa Komanso Kuzindikira Malire Anu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzitsanzira Khristu pa Nkhani Yokhala Odzichepetsa Komanso Kuzindikira Malire Anu
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • Nkhani Yofanana
  • Kudzichepetsa N’kofunika Kwambiri
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Muzikhala ndi Makhalidwe Amene Mulungu Amasangalala Nawo​—Kudzichepetsa
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
  • Kodi Tingatani Kuti Nthawi Zonse Tizikhala Odzichepetsa?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • “Nzeru Ili Ndi Odzichepetsa”
    Nsanja ya Olonda—2000
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
mwb18 September tsamba 7

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzitsanzira Khristu pa Nkhani Yokhala Odzichepetsa Komanso Kuzindikira Malire Anu

Yesu akuphunzitsa ophunzira ake kuti akhale odzichepetsa ngati kamwana

Ngakhale kuti Yesu anali munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako, anali wodzichepetsa ndipo ankazindikira malire ake popewa kulandira ulemu woyenera kupita kwa Yehova. (Yoh. 7:16-18) Koma mosiyana ndi Yesu, Satana sanali wodzichepetsa ndipo anakhala Mdyerekezi, dzina limene limatanthauza “wonenera ena zoipa.” (Yoh. 8:44) Afarisi anali ndi mtima wofanana ndi wa Satana chifukwa anali onyada ndipo ankanyoza aliyense amene ankakhulupirira Mesiya. (Yoh. 7:45-49) Kodi tingatsanzire bwanji Yesu tikapatsidwa udindo kapena utumiki winawake mumpingo?

ONERANI VIDIYO YAKUTI ‘MUZIKONDANA’​—MUZIPEWA KUCHITA NSANJE KOMANSO KUDZITAMA, MBALI YOYAMBA, KENAKO YANKHANI FUNSO LOTSATIRALI:

  • Alex akuyankhula modzikuza ndi Bill komanso Carl

    Kodi Alex anasonyeza bwanji mtima wonyada?

ONERANI VIDIYO YAKUTI ‘MUZIKONDANA’​—MUZIPEWA KUCHITA NSANJE KOMANSO KUDZITAMA, MBALI YACHIWIRI, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Alex akuyankhula modzichepetsa pamene akucheza ndi Bill ndi Carl

    Kodi Alex anasonyeza bwanji kudzichepetsa?

    Kodi Alex analimbikitsa bwanji Bill ndi Carl?

ONERANI VIDIYO YAKUTI ‘MUZIKONDANA’​—MUZIPEWA KUNYADA KOMANSO KUCHITA ZINTHU ZOSAYENERA, MBALI YOYAMBA, KENAKO YANKHANI FUNSO LOTSATIRALI:

  • M’bale Harris akusonyeza kusadzichepetsa pamene akuyankhula ndi Faye

    Kodi M’bale Harris anasonyeza bwanji kuti sankazindikira malire ake?

ONERANI VIDIYO YAKUTI ‘MUZIKONDANA’​—MUZIPEWA KUNYADA KOMANSO KUCHITA ZINTHU ZOSAYENERA, MBALI YACHIWIRI, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • M’bale Harris akusonyeza kudzichepetsa pamene akuyankhula ndi Faye

    Kodi M’bale Harris anasonyeza bwanji kuti amazindikira malire ake?

    Kodi chitsanzo chabwino cha M’bale Harris chinathandiza bwanji Faye?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena