CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AHEBERI 7-8
“Wansembe Mpaka Muyaya Monga mwa Unsembe wa Melekizedeki”
N’chifukwa chiyani tinganene kuti Melekizedeki ankaimira Yesu?
7:1—Anali mfumu komanso wansembe
7:3, 22-25—Palibe pomwe pamasonyeza kuti analowa m’malo kapenanso kulowedwa m’malo ndi munthu wina
7:5, 6, 14-17—Anachita kusankhidwa kuti akhale wansembe, osati chifukwa chobadwira m’banja la ansembe
Kodi unsembe wa Khristu umaposa bwanji wa Aroni? (it-1 1113 ¶4-5)